Salimo 1:1-6

1  Wodala+ ndi munthu amene sayenda motsatira malangizo a anthu oipa,+Saima m’njira ya anthu ochimwa,+Ndipo sakhala pansi pamodzi ndi anthu onyoza.+   Koma amakondwera ndi chilamulo cha Yehova,+Ndipo amawerenga ndi kusinkhasinkha chilamulo chake usana ndi usiku.+   Munthu ameneyo adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m’mphepete mwa mitsinje ya madzi,+Umene umabala zipatso m’nyengo yake,+Umenenso masamba ake safota,+Ndipo zochita zake zonse zidzamuyendera bwino.+   Koma oipa sali choncho.Iwo ali ngati mankhusu* amene amauluzika ndi mphepo.+   N’chifukwa chake oipa adzatsutsidwa pa chiweruzo,+Ndipo ochimwa sadzapezeka pagulu la olungama.+   Pakuti Yehova amadziwa njira za olungama,+Koma oipa adzatheratu pamodzi ndi njira zawo.+

Mawu a M'munsi

“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.