Salimo 90:1-17

Pemphero la Mose, munthu wa Mulungu woona.+ 90  Inu Yehova, ndinudi malo athu okhalamo+Ku mibadwomibadwo.+   Mapiri asanabadwe,+Kapena musanakhazikitse dziko lapansi+ ndi malo okhalapo anthu,*+Inu ndinu Mulungu kuyambira kalekale mpaka kalekale.+   Mumabwezera munthu kufumbi,+Ndipo mumanena kuti: “Bwererani kufumbi, inu ana a anthu.”+   Pakuti kwa inu zaka 1,000 zili ngati dzulo lapitali,+Ndiponso zili ngati ulonda umodzi wa usiku.*+   Mwawawonongeratu,+ ndipo amangozimiririka ngati maloto.+M’mawa amakhala ngati msipu wobiriwira umene watsitsimuka.+   Msipuwo umaphuka ndi kutsitsimuka m’mawa.+Madzulo umafota kenako umauma.+   Pakuti ife tatha chifukwa cha mkwiyo wanu,+Ndipo tasokonezeka chifukwa cha kupsa mtima kwanu.+   Zolakwa zathu mwaziika patsogolo panu,+Ndipo machimo athu obisika* ali patsogolo pa nkhope yanu yowala.+   Pakuti masiku athu onse atha chifukwa cha mkwiyo wanu.+Zaka zathu zafika kumapeto ngati mpweya wotuluka m’mphuno pousa moyo.+ 10  Masiku a moyo wathu amangokwana zaka 70,+Ndipo ngati tili ndi mphamvu yapadera amakwana zaka 80.+Koma ngakhale zili choncho, amangodzaza ndi mavuto ndi zopweteka.+Pakuti masiku amene timakhala ndi moyo amatha mwamsanga ndipo timachoka mofulumira.+ 11  Ndani angadziwe kukula kwa ukali wanu,+Ndi kukula kwa mkwiyo wanu kumene kumafanana ndi ulemu umene muyenera kulandira?+ 12  Tisonyezeni mmene tingawerengere masiku athu+Kuti tikhale ndi mtima wanzeru.+ 13  Bwererani kwa ife, inu Yehova!+ Kodi mudzatenga nthawi yaitali bwanji musanabwerere kwa ife?+Timvereni chisoni ife atumiki anu.+ 14  M’mawa mutikhutiritse ndi kukoma mtima kwanu kosatha,+Kuti tifuule mokondwera ndi kuti tikhale osangalala masiku onse a moyo wathu.+ 15  Tichititseni kusangalala kwa masiku ofanana ndi masiku amene mwatisautsa,+Kwa masiku ofanana ndi zaka zimene taona masoka.+ 16  Ntchito zanu zionekere kwa atumiki anu,+Ndipo ulemerero wanu uonekere pa ana awo.+ 17  Ubwino wa Yehova Mulungu wathu ukhale pa ife,+Ndipo mukhazikitse ntchito ya manja athu.+Muidalitse ntchito ya manja athu.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “musanamve zowawa ngati za pobereka pokhazikitsa dziko lapansi.”
Zikuoneka kuti usiku anali kuugawa zigawo zitatu za ulonda, kuyambira pamene dzuwa lalowa mpaka kutuluka. Ulonda uliwonse unali pafupifupi maola anayi malinga ndi nyengo ya pachaka.
Kapena kuti “machimo amene tinachita mosadziwa.”