Salimo 108:1-13
Nyimbo ndi Salimo la Davide.
108 Mtima wanga wakhazikika, Inu Mulungu,+Ndidzaimba nyimbo zokutamandani,+Mtima wanga udzachitanso chimodzimodzi.+
2 Iwe choimbira cha zingwe, galamuka, ndi iwenso zeze.+Ndidzadzuka m’bandakucha usanafike.+
3 Ndidzakutamandani pakati pa mitundu ya anthu, inu Yehova.+Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa mitundu ya anthu.+
4 Pakuti kukoma mtima kwanu kosatha n’kwakukulu ndipo kwafika kumwamba,+Choonadi chanu chafika kuthambo.+
5 Inu Mulungu, kwezekani kupitirira kumwamba.+Ulemerero wanu ukhale pamwamba pa dziko lonse lapansi.+
6 Kuti okondedwa anu apulumutsidwe,+Tipulumutseni ndi dzanja lanu lamanja ndi kundiyankha.+
7 Pokhala woyera, Mulungu walankhula kuti:+“Ndidzakondwa ndi kupereka Sekemu+ ngati gawo la cholowa.+Ndipo ndidzayezera anthu anga chigwa cha Sukoti.+
8 Giliyadi+ ndi wanga ndipo Manase+ ndi wanganso.Efuraimu ndi malo otetezeka a mtsogoleri amene ine ndamuika.+Yuda ndi ndodo yanga ya mtsogoleri wa asilikali.+
9 Mowabu+ ndi beseni langa losambiramo.+Ndidzaponyera Edomu+ nsapato zanga.+Ndidzafuula mosangalala+ chifukwa chogonjetsa Filisitiya.”+
10 Ndani adzandibweretsa kumzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri?+Ndani adzanditsogolera mpaka kukafika ku Edomu?+
11 Ndinu Mulungu amene mungatichititse kupambana! Koma onani tsopano mwatitaya,+Ndipo inu Mulungu wathu, simukupita kunkhondo pamodzi ndi magulu athu ankhondo.+
12 Tithandizeni kuti tichoke m’masautso,+Pakuti chipulumutso chochokera kwa munthu wochokera kufumbi n’chopanda pake.+
13 Ndi thandizo la Mulungu, tidzalandira mphamvu,+Ndipo Mulungu adzapondereza adani athu.+