Salimo 111:1-10
111 Tamandani Ya, anthu inu!+
א [ʼAʹleph]Ndidzatamanda Yehova ndi mtima wanga wonse,+ב [Behth]Pakati pa gulu+ la owongoka mtima ndi pamsonkhano wawo.+
ג [Giʹmel]
2 Ntchito za Yehova ndi zazikulu,+ד [Daʹleth]Onse amene amasangalala nazo amazisinkhasinkha.+
ה [Heʼ]
3 Zochita zake+ n’zaulemerero ndi ulemu,+ו [Waw]Ndipo chilungamo chake chidzakhalapobe kwamuyaya.+
ז [Zaʹyin]
4 Iye wakonza zoti ntchito zake zodabwitsa zizikumbukiridwa.+
ח [Chehth]Yehova ndi wachisomo ndiponso wachifundo.+
ט [Tehth]
5 Wapereka chakudya kwa anthu omuopa.+
י [Yohdh]Iye adzakumbukira pangano lake nthawi zonse.+
כ [Kaph]
6 Wafotokozera anthu ake mphamvu za ntchito zake,+ל [Laʹmedh]Mwa kuwapatsa cholowa cha mitundu ina ya anthu.+
מ [Mem]
7 Ntchito za manja ake zimadziwika ndi choonadi ndiponso chiweruzo.+נ [Nun]Malamulo onse amene amapereka ndi odalirika.+
ס [Saʹmekh]
8 Ndi ochirikizika bwino mpaka muyaya, ndithu mpaka kalekale,+ע [ʽAʹyin]Ndipo amawapereka m’choonadi ndiponso molungama.+
פ [Peʼ]
9 Wawombola anthu ake.+
צ [Tsa·dhehʹ]Wakhazikitsa pangano lake mpaka kalekale.+
ק [Qohph]Dzina lake ndi loyera ndi lochititsa mantha.+
ר [Rehsh]
10 Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova.+
ש [Sin]Onse otsatira malamulo a Mulungu ndi ozindikira.+
ת [Taw]Iye ayenera kutamandidwa mpaka muyaya.+