Salimo 3:1-8

Nyimbo ya Davide pamene anali kuthawa mwana wake Abisalomu.+ 3  Inu Yehova, n’chifukwa chiyani adani anga achuluka chotere?+N’chifukwa chiyani anthu ondiukira achuluka?+   Ponena za moyo wanga, ambiri akuti:“Mulungu sam’pulumutsa ameneyu.”+ [Seʹlah.*]   Koma inu Yehova ndinu chishango changa,+Ulemerero wanga+ ndiponso Wonditukula mutu.+   Ndidzafuulira Yehova mokweza,Ndipo iye adzandiyankha m’phiri lake loyera.+ [Seʹlah.]   Koma ine ndidzagona pansi ndi kupeza tulo.Ndidzadzuka ndithu, pakuti Yehova amandithandiza.+   Sindidzaopa anthu masauzande makumimakumiAmene andiukira ndi kundizungulira.+   Nyamukani,+ inu Yehova! Ndipulumutseni+ inu Mulungu wanga!+Pakuti mudzakantha adani anga onse pachibwano.+Mano a anthu oipa mudzawaphwanyaphwanya.+   Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.+Madalitso anu ali pa anthu anu.+ [Seʹlah.]

Mawu a M'munsi

“Seʹlah” ndi mawu achiheberi amene anali kuwagwiritsa ntchito polemba nyimbo kapena ndakatulo. Tanthauzo lake lenileni silikudziwika.