Salimo 70:1-5

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide. Nyimbo ya chikumbutso.+ 70  Inu Mulungu, fulumirani kundilanditsa,+Inu Yehova, fulumirani kundithandiza.+   Amene akufunafuna moyo wanga achite manyazi ndi kuthedwa nzeru.+Amene akukondwera ndi tsoka langa abwerere ndipo anyazitsidwe.+   Amene akunena kuti: “Eyaa! Eyaa!” abwerere chifukwa cha manyazi awo.+   Onse amene akufunafuna inu akondwere ndi kusangalala mwa inu,+Ndipo onse amene amakonda chipulumutso chanu, nthawi zonse azinena kuti: “Mulungu alemekezeke!”+   Koma ine ndasautsika ndipo ndasauka.+Inu Mulungu, chitanipo kanthu mwamsanga kuti zinthu zindiyendere bwino.+Inu ndinu thandizo langa ndi Wopereka chipulumutso kwa ine.+Inu Yehova musachedwe.+

Mawu a M'munsi