Salimo 105:1-45
105 YAMIKANI Yehova, itanani pa dzina lake,+Lengezani zochita zake pakati pa mitundu ya anthu.+
2 Muimbireni, muimbireni nyimbo zomutamanda,+Sinkhasinkhani ntchito zake zonse zodabwitsa.+
3 Nyadirani dzina lake loyera.+Mtima wa anthu ofunafuna Yehova usangalale.+
4 Funafunani Yehova ndiponso mphamvu zake.+Funafunani nkhope yake nthawi zonse.+
5 Kumbukirani ntchito zodabwitsa zimene wachita,+Kumbukirani zozizwitsa zake ndi zigamulo zotuluka m’kamwa mwake,+
6 Inu mbewu ya Abulahamu mtumiki wake,+Inu ana a Yakobo, osankhidwa mwapadera.+
7 Iye ndi Yehova Mulungu wathu.+Zigamulo zake zili padziko lonse lapansi.+
8 Wakumbukira pangano lake mpaka kalekale,+Wakumbukira lonjezo limene anapereka ku mibadwo 1,000,+
9 Wakumbukira pangano limene anapangana ndi Abulahamu,+Ndi lonjezo limene analumbira kwa Isaki,+
10 Lonjezo limeneli analikhazikitsa monga lamulo kwa Yakobo,Monga pangano lokhalapo mpaka kalekale kwa Isiraeli,+
11 Pamene anati: “Ndidzakupatsa dziko la Kanani+Kuti likhale gawo la cholowa chako.”+
12 Pamene ananena zimenezi, n’kuti iwo ali ochepa.+N’kuti ali ochepa kwambiri komanso ali alendo m’dzikolo.+
13 Iwo anapitiriza kuyendayenda pakati pa mitundu yosiyanasiyana,+Anali kuchoka mu ufumu wina ndi kupita kukakhala ndi anthu a mtundu wina.+
14 Mulungu sanalole kuti munthu aliyense awachitire zachinyengo,+Koma anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo.+
15 Iye anati: “Anthu inu musakhudze odzozedwa anga,+Ndipo aneneri anga musawachitire choipa chilichonse.”+
16 Iye anadzetsa njala yaikulu m’dzikomo,+Ndipo anathyola ndodo zonse zopachikapo mkate wozungulira woboola pakati.+
17 Mulungu anatsogoza munthu kuti anthu akewo abwere pambuyo pake,Anatumiza Yosefe amene anagulitsidwa kuti akhale kapolo.+
18 Kumeneko anasautsa mapazi ake ndi matangadza,+Anam’manga ndi maunyolo.+
19 Mawu a Yehova anamuyenga,+Kufikira pamene lonjezo la Mulungu linakwaniritsidwa.+
20 Mfumu inalamula kuti amutulutse m’ndende.+Wolamulira mitundu ya anthu analamula kuti Yosefe amasulidwe.
21 Anamuika kukhala mkulu woyang’anira banja lake,+Komanso wolamulira chuma chake chonse.+
22 Anamupatsa ulamuliro womanga kalonga aliyense wa mfumu,+Komanso kuphunzitsa zinthu za nzeru anthu achikulire.+
23 Kenako Isiraeli anapita ku Iguputo,+Yakobo anakhala monga mlendo m’dziko la Hamu.+
24 Mulungu anachititsa anthu ake kuberekana,+Ndipo pang’onopang’ono anawasandutsa anthu amphamvu kuposa adani awo.+
25 Analola adaniwo kusintha mitima yawo ndi kudana ndi anthu ake,+Anawalola kuchitira atumiki ake zachinyengo.+
26 Ndiyeno anatumiza Mose mtumiki wake,+Ndi Aroni amene anamusankha.+
27 Iwowa anasonyeza Aiguputo zizindikiro za Mulungu,+Ndi zozizwitsa m’dziko la Hamu.+
28 Anatumiza mdima moti kunada.+Ndipo iwo sanapandukire mawu ake.+
29 Anasandutsa madzi awo kukhala magazi,+Ndipo anapha nsomba zawo.+
30 M’dziko lawo munadzaza achule,+Chimodzimodzinso m’zipinda za mafumu awo.
31 Analamula kuti pagwe tizilombo touluka toyamwa magazi,+Komanso ntchentche zoluma m’madera awo onse.+
32 Anawagwetsera matalala m’malo mwa mvula,+Anawagwetseranso moto woyaka, walawilawi m’dziko lawo.+
33 Anawononga mitengo yawo ya mpesa ndi ya mkuyu,Ndipo anakhadzula mitengo m’dziko lawo.+
34 Analamula kuti pagwe dzombe,+Ndipo panagwa dzombe losawerengeka la mtundu winawake.+
35 Dzombelo linadya zomera zonse m’dziko lawo.+Linadyanso mbewu zonse za m’munda mwawo.
36 Mulungu anapha mwana aliyense woyamba kubadwa m’dziko lawo,+Chiyambi cha mphamvu zawo zonse zobereka.+
37 Ndiyeno anayamba kuwatulutsa atatenga siliva ndi golide.+Pakati pa mafuko ake panalibe amene anapunthwa panjira.
38 Aiguputo anasangalala pamene Aisiraeli anatuluka m’dzikolo,Pakuti anali kuwaopa kwambiri.+
39 Mulungu anayala mtambo kuti uziwatchinga,+Ndipo anawapatsa moto kuti uziwaunikira usiku.+
40 Anapempha nyama ndipo anawapatsa zinziri,+Anawadyetsa chakudya chochokera kumwamba.+
41 Anatsegula thanthwe ndipo panatuluka madzi ambiri.+Madziwo anayenda ngati mtsinje kudutsa m’dera lopanda madzi.+
42 Iye anakumbukira lonjezo lake loyera limene analonjeza mtumiki wake Abulahamu.+
43 Choncho Mulungu anatulutsa anthu ake m’dzikomo anthuwo akusangalala,+Anatulutsa osankhidwa ake akufuula mokondwera.+
44 Pang’onopang’ono anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina,+Ndipo zipatso za ntchito imene mitundu ya anthu inagwira mwakhama, anazitenga kukhala zawo,+
45 Anachita zimenezi kuti asunge malangizo ake,+Ndi kusunga malamulo ake.+Tamandani Ya, anthu inu!+