Salimo 43:1-5

43  Ndiweruzeni+ inu Mulungu,Weruzani mlandu wanga+ motsutsana ndi mtundu wosakhulupirika.Ndipulumutseni kwa munthu wachinyengo ndi wochita zosalungama.+   Pakuti inu ndinu Mulungu wanga, ndinu malo anga achitetezo.+N’chifukwa chiyani mwanditaya?Ndikuyenderanji wachisoni chifukwa choponderezedwa ndi mdani wanga?+   Tumizani kuwala kwanu ndi choonadi chanu.+Zimenezi zinditsogolere.+Zindifikitse kuphiri lanu lopatulika ndi kuchihema chanu chachikulu.+   Ndidzapita paguwa lansembe la Mulungu,+Kwa Mulungu amene amandikondweretsa ndi kundisangalatsa.+Ndipo ndidzakutamandani ndi zeze, inu Mulungu, Mulungu wanga.+   N’chifukwa chiyani ukutaya mtima, moyo wangawe?+Ndipo n’chifukwa chiyani ukusautsika mkati mwanga?Yembekezera Mulungu,+Ndipo ndidzamutamanda pakuti iye ndiye mpulumutsi wanga wamkulu ndi Mulungu wanga.+

Mawu a M'munsi