Salimo 17:1-15

Pemphero la Davide. 17  Imvani dandaulo lolungama, inu Yehova. Mvetserani kulira kwanga kochonderera.+Tcherani khutu ku pemphero langa limene likutuluka pamilomo yopanda chinyengo.+   Chiweruzo changa chichokere kwa inu.+Maso anu aone kuwongoka mtima kwanga.+   Mwasanthula mtima wanga, mwandifufuza usiku,+Ndipo mwandiyenga. Mudzaona kuti sindinaganizire kuchita choipa chilichonse.+Pakamwa panga sipadzaphwanya malamulo.+   Kunena za ntchito za anthu,Ndakhala wosamala mwa kusunga mawu a pakamwa panu, kuti ndisatengere njira ya wachifwamba.+   Mapazi anga ayendebe m’njira zanu,+Mmene sadzapunthwa ngakhale pang’ono.+   Ine ndikuitana pa inu, chifukwa mudzandiyankha, inu Mulungu.+Tcherani khutu kwa ine. Imvani mawu anga.+   Sonyezani kukoma mtima kosatha mwa kuchita zodabwitsa,+ inu Mpulumutsi wa anthu othawira kwa inu,Amene akuthawa anthu ogalukira dzanja lanu lamanja.+   Ndisungeni monga mwana wa diso,+Ndibiseni mumthunzi wa mapiko anu,+   Chifukwa cha anthu oipa amene akundipondereza.Adani a moyo wanga atsala pang’ono kundipeza.+ 10  Mitima yawo siimva chisoni,*+Ndipo amalankhula modzikuza ndi pakamwa pawo.+ 11  Tsopano adaniwo atizungulira, kulikonse kumene tingapite.+Akutiyang’anitsitsa kuti atigwetse.+ 12  Aliyense wa iwo akuoneka ngati mkango umene ukufunitsitsa kukhadzula nyama.+Akuonekanso ngati mkango wamphamvu umene wabisalira nyama. 13  Nyamukani, inu Yehova, yang’anizanani naye maso ndi maso woipayo.+M’gonjetseni. Pulumutsani moyo wanga kwa woipayo ndi lupanga lanu.+ 14  Ndipulumutseni kwa anthu ndi dzanja lanu, inu Yehova,+Ndipulumutseni kwa anthu a m’nthawi* ino,+ amene gawo lawo lili m’moyo uno.+Anthu amene mimba zawo mwazidzaza ndi chuma chanu chobisika,+Amene ali ndi ana aamuna ochuluka,+Ndipo amakundikira ana awo chuma.+ 15  Koma ine ndidzaona nkhope yanu m’chilungamo.+Podzuka, ndidzakhutira pokuonani.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “adzikuta ndi mafuta awo omwe.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.