Salimo 51:1-19
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. Pa nthawi imene mneneri Natani anapita kwa Davide atagona ndi Bati-seba.+
51 Ndikomereni mtima inu Mulungu, malinga ndi kukoma mtima kwanu kosatha.+Malinga ndi kuchuluka kwa chifundo chanu, fafanizani zolakwa zanga.+
2 Mundisambitse bwinobwino ndi kuchotsa cholakwa changa,+Ndiyeretseni ku tchimo langa.+
3 Pakuti zolakwa zanga ndikuzidziwa bwino,+Ndipo tchimo langa lili pamaso panga nthawi zonse.+
4 Ine ndakuchimwirani kwambiri,+Ndipo ndachita chinthu choipa pamaso panu,+Choncho mukamalankhula mumalankhula zachilungamo,+Ndipo mukamaweruza, mumaweruza molungama.+
5 Taonani! Anandilandira mu zowawa za pobereka ndili wochimwa.+Ndipo ndine wochimwa kuchokera pamene mayi anga anatenga pakati panga.+
6 Taonani! Mumakondwera ndi choonadi chochokera pansi pa mtima.+Ndipo mundidziwitse nzeru mumtima mwanga.+
7 Ndiyeretseni ndi hisope ku machimo anga kuti ndikhale woyera.+Ndisambitseni kuti ndiyere kwambiri kuposa chipale chofewa.+
8 Ndichititseni kumva kufuula kokondwera ndi kosangalala,+Kuti munthu* amene mwamuthyola akondwere.+
9 Ndikhululukireni machimo anga,+Ndipo fafanizani zolakwa zanga zonse.+
10 Inu Mulungu, lengani mtima wolungama mkati mwanga,+Ndipo ikani maganizo* atsopano ndi okhazikika mwa ine.+
11 Musandichotse pamaso panu ndi kunditaya.+Ndipo musandichotsere mzimu wanu woyera.+
12 Bwezeretsani mwa ine chisangalalo chifukwa cha chipulumutso chanu,+Ndichirikizeni ndi mzimu wofunitsitsa.+
13 Anthu ophwanya malamulo ndidzawaphunzitsa njira zanu,+Kuti ochimwa abwerere kwa inu.+
14 Inu Mulungu, ndilanditseni ku mlandu wa magazi,+ inu Mulungu wa chipulumutso changa,+Kuti lilime langa linene za chilungamo chanu mokondwera.+
15 Inu Yehova, tsegulani milomo yangayi,+Kuti pakamwa panga patamande inu.+
16 Pakuti nsembe singakusangalatseni, chifukwa ikanakusangalatsani ndikanaipereka kwa inu.+Nsembe yopsereza yathunthu singakusangalatseni.+
17 Kudzimvera chisoni mumtima ndizo nsembe zimene Mulungu amavomereza.+Inu Mulungu, simudzanyoza mtima wosweka ndi wophwanyika.+
18 Chitirani Ziyoni zabwino mwa kukoma mtima kwanu.+Ndipo mangani mpanda wa Yerusalemu.+
19 Mukatero mudzakondwera ndi nsembe zachilungamo,+Mudzakondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zathunthu.+Pamenepo ng’ombe zamphongo zidzaperekedwa paguwa lanu la nsembe.+