Salimo 62:1-12
Kwa wotsogolera nyimbo pa Yedutuni.* Nyimbo ya Davide.
62 Ndithudi, moyo wanga ukuyembekezera Mulungu modekha.+Chipulumutso changa chidzachokera kwa iye.+
2 Iye ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, malo anga okwezeka ndiponso achitetezo.+Sindidzagwedezeka kwambiri.+
3 Kodi mudzayesayesa kufikira liti kuti muphe munthu amene mumadana naye?+Nonsenu muli ngati khoma lopendekeka, khoma lamiyala limene akulikankha kuti ligwe.+
4 Iwo amapatsa munthu malangizo kuti amukope ndi kumutsitsa pamalo ake aulemu.+Bodza limawasangalatsa.+Iwo amadalitsa ndi pakamwa pawo, koma mumtima mwawo amatemberera.+ [Seʹlah.]
5 Ndithudi, yembekezera Mulungu modekha, iwe moyo wanga,+Chifukwa chiyembekezo changa chichokera kwa iye.+
6 Ndithudi, iye ndi thanthwe langa ndi chipulumutso changa, malo anga okwezeka ndiponso achitetezo.+Sindidzagwedezeka.+
7 Chipulumutso ndi ulemerero wanga zili mwa Mulungu.+Iye ndi thanthwe langa lolimba ndi malo anga othawirako.+
8 Mukhulupirireni nthawi zonse, anthu inu.+Mukhuthulireni za mumtima mwanu.+Mulungu ndiye pothawirapo pathu.+ [Seʹlah.]
9 Ndithudi, ana a anthu ochokera kufumbi ali ngati mpweya,+Ana a anthu ndi malo othawirako achinyengo.+Onse pamodzi akaikidwa pasikelo ndi opepuka kuposa mpweya.+
10 Musadalire chizolowezi chobera ena mwachinyengo,+Ndipo musakhale wachabechabe chifukwa chochita uchifwamba.+Ngati chuma chanu chachuluka, mtima wanu wonse usakhale pachumacho.+
11 Kawiri konse ndamva kuti Mulungu wanena kuti,+Mphamvu ndi za Mulungu.+
12 Komanso kukoma mtima kosatha ndi kwanu, inu Yehova,+Pakuti inu mumabwezera aliyense mogwirizana ndi ntchito zake.+