Salimo 7:1-17

Nyimbo yoimba polira* imene Davide anaimbira Yehova, yonena za mawu a Kusi M’benjamini. 7  Inu Yehova Mulungu wanga,+ ine ndathawira kwa inu.+Ndipulumutseni kwa onse ondizunza ndipo mundilanditse,+   Kuti pasapezeke wondikhadzulakhadzula ngati mmene mkango umachitira,+Pasapezeke wondikwatula popanda wondilanditsa.+   Inu Yehova Mulungu wanga, ngati ndachita cholakwa chilichonse,+Ngati manja anga achita zosalungama zilizonse,+   Ngati munthu wondichitira zabwino ndamubwezera zoipa,+Kapena ngati ndafunkha zinthu za aliyense wondichitira zoipa amene sanaphule kanthu,+   Mdani wanga afunefune moyo wanga,+Ndipo aupeze ndi kuupondaponda pafumbi.Ulemerero wanga aukwirire m’fumbi. [Seʹlah.]   Nyamukani, inu Yehova, mu mkwiyo wanu.+Imirirani ndi kukhaulitsa amene andisonyeza mkwiyo ndi kundichitira zoipa.+Dzukani ndi kundithandiza,+ pakuti mwalamula kuti chiweruzo chiperekedwe.+   Mitundu ya anthu isonkhane ndi kukuzungulirani,Ndipo inu mubwerere kumwamba ndi kuwakhaulitsa.   Yehova adzapereka chigamulo ku mitundu ya anthu.+Ndiweruzeni inu Yehova, mogwirizana ndi chilungamo changa,+Komanso mogwirizana ndi mtima wanga wosagawanika.+   Chonde, thetsani kuipa kwa anthu oipa,+Ndipo khazikitsani wolungama.+Mulungu pokhala wolungama+ akuyesa mtima+ ndi impso.+ 10  Chishango changa chili ndi Mulungu,+ Mpulumutsi wa anthu owongoka mtima.+ 11  Mulungu ndi Woweruza wolungama,+Ndipo Mulungu amapereka ziweruzo tsiku lililonse. 12  Ngati munthu sadzabwerera kusiya zoipa,+ Mulungu adzanola lupanga lake,+Adzakunga uta wake ndi kukonzekera kulasa.+ 13  Iye adzadzikonzera zida za imfa,+Ndipo adzapanga mivi yake kukhala yoyaka moto walawilawi.+ 14  Taonani! Wina ali ndi pakati pa zinthu zoipa,+Watenga pakati pa mavuto ndipo ndithu adzabereka chinyengo.+ 15  Iye wafukula dzenje, walikumbadi.+Koma adzagwera m’dzenje lokumba yekha.+ 16  Mavuto ake adzabwerera pamutu pake,+Ndipo chiwawa chake chidzatsikira paliwombo pake.+ 17  Ndidzatamanda Yehova chifukwa cha chilungamo chake.+Ndidzaimba nyimbo motsatizana ndi zipangizo zoimbira, kutamanda dzina+ la Yehova Wam’mwambamwamba.+

Mawu a M'munsi

Tanthauzo la mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “nyimbo yoimba polira” silikudziwika, koma mwina mawu amenewo angatanthauze nyimbo yoimba mokhudzidwa mtima kwambiri. Kaimbidwe kake kangasonyeze kuti moyo wa munthuyo uli pangozi, akufuula kupempha thandizo, kapena akukondwera ndipo akutamanda winawake.