Salimo 69:1-36
Kwa wotsogolera nyimbo pa Maluwa.*+ Salimo la Davide.
69 Ndipulumutseni, inu Mulungu, pakuti madzi afika m’khosi.+
2 Ndamila m’matope akuya, mmene mulibe malo oponda.+Ndalowa m’madzi akuya,Ndipo mtsinje wa madzi othamanga wandikokolola.+
3 Ndatopa ndi kufuula kwanga,+Mawu asasa pammero panga.Maso anga achita mdima poyembekezera Mulungu wanga.+
4 Anthu amene amadana nane popanda chifukwa achuluka kuposa tsitsi la m’mutu mwanga.+Amene akufuna kunditsitsira kuli chete, chifukwa chodana nane popanda chifukwa, achuluka kwambiri.+Ngakhale kuti sindine wakuba, anandikakamiza kubweza zinthu zimene zinabedwa.
5 Inu Mulungu, mwadziwa kupusa kwanga,Ndipo kupalamula kwanga sikunabisike kwa inu.+
6 Onse amene akuyembekezera inu asachite manyazi chifukwa cha ine,+Inu Ambuye Wamkulu Koposa, Yehova wa makamu.+Onse amene akufunafuna inu, asanyazitsidwe chifukwa cha ine,+Inu Mulungu wa Isiraeli.+
7 Ine ndanyamula chitonzo chifukwa cha inu,+Manyazi aphimba nkhope yanga.+
8 Ndadzipatula pakati pa abale anga,+Ndipo ndakhala mlendo pakati pa ana aamuna a mayi anga.+
9 Pakuti kudzipereka kwambiri panyumba yanu kwandidya,+Ndipo mnyozo wa anthu amene akukutonzani wagwa pa ine.+
10 Ndipo ndinalira ndi kusala kudya chifukwa cha moyo wanga,+Koma anthu anali kungonditonza chifukwa cha zimenezo.+
11 Pamene ndinavala ziguduli,Ndinakhala ngati mwambi kwa iwo.+
12 Anthu okhala kuchipata anayamba kundidera nkhawa,+Ndipo anthu amene anali kumwa zakumwa zoledzeretsa anali kundinena mu nyimbo zawo.+
13 Koma ine ndinali kupemphera kwa inu Yehova,+Pa nthawi yovomerezedwa, inu Mulungu.+Ndiyankheni mwa kuchuluka kwa kukoma mtima kwanu kosatha, ndipo sonyezani kuti ndinudi mpulumutsi.+
14 Ndipulumutseni m’matope kuti ndisamire.+Ndipulumutseni kwa anthu odana nane+ ndiponso ku madzi akuya.+
15 Musalole kuti mtsinje wa madzi othamanga undikokolole,+Kapena kuti madzi akuya andimize,Kapenanso kuti dzenje* lindimeze ndi kutseka pakamwa pake.+
16 Ndiyankheni inu Yehova, pakuti kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwabwino.+Ndicheukireni chifukwa chifundo chanu ndi chochuluka,+
17 Ndipo ine mtumiki wanu musandibisire nkhope yanu.+Ndiyankheni mwamsanga, chifukwa ndasautsika kwambiri.+
18 Yandikirani moyo wanga ndi kuupulumutsa.+Ndiwomboleni kwa adani anga.+
19 Inu mwadziwa chitonzo changa, manyazi anga ndi kunyazitsidwa kwanga.+Onse odana nane ali pamaso panu.+
20 Mtima wanga wasweka chifukwa cha chitonzo, ndipo chilonda chake ndi chosachiritsika.+Ndinali kuyembekezera kuti wina andimvere chifundo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe,+Ndinali kuyembekezera onditonthoza, koma sanapezeke ngakhale mmodzi.+
21 Koma anandipatsa chomera chakupha kuti ndidye,+Ndipo anayesa kundimwetsa vinyo wowawasa pamene ndinali ndi ludzu.+
22 Tebulo lawo likhale msampha,+Ndipo akodwe ndi chilichonse chimene akusangalala nacho.+
23 Maso awo achite mdima kuti asaone,+Ndipo chititsani miyendo* yawo kunjenjemera mosalekeza.+
24 Atsanulireni matemberero anu,+Ndipo mkwiyo woyaka moto uwagwere.+
25 Msasa wawo wokhala ndi mpanda ukhale bwinja,+Ndipo m’mahema awo musapezeke munthu wokhalamo.+
26 Pakuti iwo amalondalonda munthu amene inu mwamulanga,+Ndipo amakamba za ululu wa anthu amene inu mwawalasa.
27 Wonjezerani zolakwa pa zolakwa zawo,+Ndipo inu musawaone monga olungama.+
28 Afafanizidwe m’buku la anthu amoyo,+Ndipo iwo asalembedwe m’bukumo pamodzi ndi anthu olungama.+
29 Koma ine ndasautsika ndipo ndikumva kupweteka.+Inu Mulungu, chipulumutso chanu chinditeteze.+
30 Ndidzatamanda dzina la Mulungu mwa kuimba nyimbo,+Ndipo ndidzamulemekeza ndi nyimbo zomuyamika.+
31 Zimenezinso zidzasangalatsa kwambiri Yehova kuposa ng’ombe yamphongo,+Kuposa ng’ombe yamphongo yaing’ono imene ili ndi nyanga, komanso yogawanika ziboda.+
32 Anthu ofatsa adzaona zimenezi ndipo adzakondwera.+Inu amene mukutumikira Mulungu, mtima wanu ukhalenso ndi moyo.+
33 Pakuti Yehova akumvetsera osauka,+Ndipo sadzanyoza anthu ake amene ali m’ndende.+
34 Kumwamba ndi dziko lapansi zimutamande,+Chimodzimodzinso nyanja ndi chilichonse choyenda mmenemo.+
35 Pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyoni,+Ndipo adzamanga mizinda ya Yuda,+Iwo adzakhala mmenemo ndi kutenga dzikolo kukhala lawo.+
36 Ana a atumiki ake adzalandira dzikolo monga cholowa chawo,+Ndipo anthu okonda dzina lake adzakhala mmenemo.+