Salimo 63:1-11

Nyimbo ya Davide pamene anali m’chipululu cha Yuda.+ 63  Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ine ndikukufunafunani.+Moyo wanga ukulakalaka inu.+Thupi langa lalefuka chifukwa cholakalaka inuM’dziko louma ndi lopanda chonde, lopanda madzi.+   Choncho ndakuonani m’malo oyera,+Chifukwa ndaona mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.+   Pakuti kukoma mtima kwanu kosatha n’kwabwino kuposa moyo,+Milomo yanga idzakuyamikirani.+   Choncho ndidzakutamandani pa nthawi yonse ya moyo wanga.+Ndidzapemphera m’dzina lanu nditakweza manja anga.+   Moyo wanga wakhutira ndi gawo labwino kwambiri, wakhutira ndi zinthu zabwino kwambiri,+Ndipo milomo yanga ikukutamandani ndi mfuu yachisangalalo.+   Ndikakumbukira inu ndili pabedi langa,+Pa nthawi za ulonda wa usiku* ndimasinkhasinkha za inu.+   Pakuti mwandithandiza,+Ndipo mumthunzi wa mapiko anu ndimafuula mosangalala.+   Ndakulondolani kulikonse,+Dzanja lanu lamanja landigwira mwamphamvu.+   Koma ofuna kuwononga moyo wanga,+Adzatsikira kumanda.+ 10  Adzaphedwa ndi lupanga,+Adzakhala chakudya cha nkhandwe.+ 11  Ndipo mfumu idzakondwera mwa Mulungu.+Aliyense wolumbira m’dzina la Mulungu adzam’tamanda,+Pakuti pakamwa pa anthu olankhula chinyengo padzatsekedwa.+

Mawu a M'munsi

Pa nthawi ya Mfumu Davide, Aisiraeli anali ndi maulonda a usiku atatu. Ulonda woyamba unkayamba 6 koloko madzulo mpaka 10 koloko usiku. Ulonda wachiwiri unkayamba 10 koloko usiku mpaka 2 koloko usiku, ndipo ulonda wachitatu unkayamba 2 koloko usiku mpaka 6 koloko m’mawa.