Salimo 77:1-20
Kwa wotsogolera nyimbo pa Yedutuni. Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+
77 Ndidzafuulira Mulungu,+Ndithu, ndidzafuulira Mulungu, ndipo iye adzatchera khutu lake kwa ine.+
2 Pa tsiku la zowawa zanga ndafunafuna Yehova.+Ndakweza dzanja langa kumwamba usiku wonse, ndipo silinachite dzanzi.Koma sindinatonthozeke.+
3 Ndidzakumbukira Mulungu ndipo ndidzavutika maganizo.+Ine ndasautsika. N’chifukwa chake ndafooka.+ [Seʹlah.]
4 Mwatsegula zikope zanga,+Ndipo ndavutika mtima, moti sindingathe kulankhula.+
5 Ndaganizira za masiku akale,+Ndaganizira zaka za makedzana.
6 Usiku ndidzakumbukira nyimbo zanga zoimbidwa ndi chipangizo cha zingwe.+Ndidzasonyeza kudera nkhawa mumtima mwanga,+Ndipo ndidzasinkhasinkha zinthu zonse mozama.
7 Kodi Yehova watitaya mpaka kalekale?+Kodi sitidzathanso kumusangalatsa?+
8 Kodi kukoma mtima kwake kosatha wakusiya mpaka muyaya?+Kodi malonjezo ake sadzakwaniritsidwa+ ku mibadwomibadwo?
9 Kodi Mulungu waiwala kukhala wokoma mtima,+Kapena watsekereza chifundo chake mwaukali?+ [Seʹlah.]
10 Kodi ndizingonena kuti: “Zimene zikundisautsa n’zakuti,+Wam’mwambamwamba wasiya kutipatsa thandizo”?+
11 Ndidzakumbukira zochita za Ya,+Ndithu ndidzakumbukira ntchito yanu yodabwitsa yakale.+
12 Ndidzasinkhasinkha za ntchito zanu zonse,+Ndipo ndiziganizira zochita zanu.+
13 Inu Mulungu, njira yanu ili m’malo oyera.+Kodi ndi Mulungu wamkulu uti amene angafanane ndi Mulungu wathu?+
14 Inu ndinu Mulungu woona amene mukuchita zodabwitsa.+Mphamvu zanu mwazidziwikitsa pakati pa mitundu ya anthu.+
15 Ndi dzanja lanu mwawombola anthu anu,+Ana aamuna a Yakobo ndi Yosefe. [Seʹlah.]
16 Madzi akuonani, inu Mulungu,Madzi akuonani, ndipo ayamba kumva ululu woopsa.+Komanso madzi akuya ayamba kuwinduka.+
17 Mitambo yatulutsa mabingu ndi kugwetsa madzi.+Thambo latulutsa mkokomo.Mphezi zanu zinawala paliponse ngati mivi.+
18 Phokoso la bingu lanu linali ngati la mawilo a galeta.+Mphezi zinaunika padziko.+Ndipo dziko lapansi linagwedezeka ndi kuyamba kunjenjemera.+
19 Msewu wanu unadutsa panyanja,+Ndipo njira yanu inadutsa pamadzi ambiri.Mmene mapazi anu anaponda simunaoneke.
20 Mwatsogolera anthu anu ngati nkhosa,+Kudzera mwa Mose ndi Aroni.+