Salimo 126:1-6
Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
126 Pamene Yehova anasonkhanitsa ndi kubwezeretsa ogwidwa ukapolo a Ziyoni,+Tinakhala ngati tikulota.+
2 Pa nthawiyo tinaseka kwambiri,+Ndipo lilime lathu linatulutsa mawu okondwa.+Pamenepo anthu a mitundu ina anayamba kuuzana kuti:+“Yehova wachitira anthu amenewa zinthu zazikulu.”+
3 Yehova watichitira zazikulu.+Tasangalala.+
4 Sonkhanitsani ndi kubwezeretsa gulu lathu logwidwa ukapolo inu Yehova,+Ngati mmene mumabwezeretsera madzi m’mitsinje ya ku Negebu.+
5 Amene akukhetsa misozi pofesa mbewu,+Adzakolola akufuula mosangalala.+
6 Amene akupita kumunda akulira,+Atasenza thumba lodzaza mbewu,+Adzabwerako akufuula mosangalala,+Atasenza mtolo wake wa zokolola.+