Salimo 83:1-18
Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+
83 Inu Mulungu, musakhale chete.+Musakhale phee osalankhulapo kanthu ndipo musakhale duu osachitapo kanthu, inu Mulungu.+
2 Taonani! Adani anu akuchita phokoso.+Anthu odana nanu kwambiri atukula mitu yawo.+
3 Iwo amakumana mwachinsinsi kuti akambirane zochitira chiwembu anthu anu.+Ndipo amakonzera chiwembu anthu anu obisika.+
4 Iwo anena kuti: “Bwerani tiwafafanize kuti asakhalenso mtundu,+Ndi kuti dzina la Isiraeli lisakumbukikenso.”+
5 Pakuti ndi mtima wonse, iwo amagawana nzeru,+Ndipo anapangana pangano lotsutsana ndi inu.+
6 Amenewa ndi anthu okhala m’mahema a Edomu+ ndi m’mahema a Isimaeli, Amowabu+ ndi Ahagara,+
7 Agebala, Aamoni,+ Aamaleki,Afilisiti+ pamodzi ndi anthu a ku Turo.+
8 Asuri nawonso agwirizana nawo,+Ndipo amapereka thandizo kwa ana aamuna a Loti.+ [Seʹlah.]
9 Muwachitire zimene munachitira Midiyani+ ndi Sisera.+Muwachitirenso zimene munachitira Yabini+ kuchigwa cha Kisoni.+
10 Iwo anawonongedwa ku Eni-dori.+Anasanduka manyowa a m’nthaka.+
11 Atsogoleri awo muwachititse kukhala ngati Orebi ndi Zeebi.+Ndipo mafumu awo onse muwachititse kukhala ngati Zeba ndi Zalimuna.+
12 Iwo anena kuti: “Tiyeni tilande malo amene Mulungu amakhalako kuti akhale athu.”+
13 Inu Mulungu wanga, achititseni kukhala ngati udzu wouma wouluzika ndi mphepo,+Ngati mapesi otengeka ndi mphepo.+
14 Mofanana ndi moto wotentha nkhalango,+Ndiponso malawi a moto woyaka m’mapiri,+
15 Muwathamangitse ndi mphepo yanu yamphamvu,+Ndipo muwasokoneze ndi mphepo yanu yamkuntho.+
16 Achititseni manyazi,+Kuti anthu afunefune dzina lanu, inu Yehova.+
17 Achite manyazi ndi kusokonezeka nthawi zonse.+Athedwe nzeru ndi kutheratu,+
18 Kuti anthu adziwe+ kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova,+Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba,+ wolamulira dziko lonse lapansi.+