Salimo 34:1-22
Salimo la Davide, pa nthawi imene anachita zinthu ngati wamisala+ pamaso pa Abimeleki* moti anam’pitikitsa ndipo Davideyo anathawa.
א [ʼAʹleph]
34 Ndidzatamanda Yehova nthawi zonse.+Ndidzamutamanda ndi pakamwa panga mosalekeza.+
ב [Behth]
2 Ndidzadzitamandira mwa Yehova.+Ofatsa adzamva ndi kukondwera.+
ג [Giʹmel]
3 Lemekezani Yehova pamodzi ndi ine+ anthu inu,Tiyeni tonse tikweze dzina lake.+
ד [Daʹleth]
4 Ndinafunsa kwa Yehova ndipo iye anandiyankha,+Pakuthawathawa kwanga konse iye anandilanditsa.+
ה [Heʼ]
5 Amene anamukhulupirira anasangalala,+Ndipo nkhope zawo sizinachite manyazi.+
ז [Zaʹyin]
6 Wosautsikayu anaitana ndipo Yehova anamva.+Anamupulumutsa m’masautso ake onse.+
ח [Chehth]
7 Mngelo wa Yehova amamanga msasa mozungulira onse oopa Mulungu,+Ndipo amawapulumutsa.+
ט [Tehth]
8 Anthu inu, talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino.+Wodala ndi munthu wamphamvu amene amathawira kwa iye.+
י [Yohdh]
9 Opani Yehova, inu oyera ake,+Pakuti onse omuopa sasowa kanthu.+
כ [Kaph]
10 Mikango yamphamvu ingakhale ndi chakudya chochepa ndipo ingamve njala.+Koma ofunafuna Yehova sadzasowa chilichonse chabwino.+
ל [Laʹmedh]
11 Bwerani kuno ana anga, ndimvetsereni.+Ndikuphunzitsani kuopa Yehova.+
מ [Mem]
12 Kodi munthu wokonda moyo ndani,+Amene akufuna kukhala ndi moyo wabwino kwa masiku ambiri?+
נ [Nun]
13 Tetezani lilime lanu ku zinthu zoipa,+Ndi milomo yanu kuti isalankhule chinyengo.+
ס [Saʹmekh]
14 Patukani pa zinthu zoipa ndipo chitani zabwino.+Funafunani mtendere ndi kuusunga.+
ע [ʽAʹyin]
15 Maso a Yehova ali pa olungama,+Ndipo makutu ake amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.+
פ [Peʼ]
16 Nkhope ya Yehova imakwiyira anthu ochita zoipa,+Kuti dzina lawo lisatchulidwenso padziko lapansi.+
צ [Tsa·dhehʹ]
17 Olungama anafuula, ndipo Yehova anamva,+Iye anawapulumutsa m’masautso awo onse.+
ק [Qohph]
18 Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka.+Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.+
ר [Rehsh]
19 Masoka a munthu wolungama ndi ochuluka,+Koma Yehova amamupulumutsa ku masoka onsewo.+
ש [Shin]
20 Amateteza mafupa onse a wolungamayo.Ndipo palibe fupa ngakhale limodzi limene lathyoledwa.+
ת [Taw]
21 Masoka adzapha munthu woipa.+Ndipo wodana ndi munthu wolungama adzapezeka wolakwa.+
22 Yehova amawombola moyo wa atumiki ake.+Ndipo palibe aliyense wothawira kwa iye amene adzapezeka wolakwa.+