Salimo 22:1-31
Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe motsatira Mbawala Yaikazi ya M’bandakucha. Nyimbo ya Davide.
22 Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?+N’chifukwa chiyani mukuchedwa kundipulumutsa?+N’chifukwa chiyani simukumva mawu a kubuula kwanga?+
2 Inu Mulungu wanga, ine ndimaitana usana koma simundiyankha.+Usiku ndimaitanabe, moti sindikukhala chete.+
3 Koma inu ndinu woyera.+Mukukhala pakati pa zitamando za Isiraeli.+
4 Makolo athu anali kudalira inu.+Iwo anali kudalira inu ndipo munali kuwapulumutsa.+
5 Iwo anali kufuulira inu,+ ndipo anali kupulumuka.+Anali kudalira inu, ndipo simunawachititse manyazi.+
6 Koma ine ndine nyongolotsi+ osati munthu.Anthu amanditonza ndipo ndine wonyozeka kwa anthu.+
7 Anthu onse ondiona amandinyodola.+Iwo amandinyogodola ndi pakamwa pawo, ndipo amapukusa mitu yawo mondinyoza.+ Iwo amati:
8 “Anadzipereka kwa Yehova.+ Amupulumutse Iyeyo!+Ngati Mulungu amamukonda, amulanditse!”+
9 Pakuti ndinu amene munanditulutsa m’mimba,+Amene munandichititsa kumva kuti ndine wotetezeka pamene ndinali kuyamwa mabere a mayi anga.+
10 Ndinaponyedwa m’manja mwanu kuchokera m’mimba.+Kuyambira ndili m’mimba mwa mayi anga, inu mwakhala Mulungu wanga.+
11 Musakhale kutali ndi ine, chifukwa zondisautsa zili pafupi,+Ndiponso chifukwa ndilibe mthandizi winanso.+
12 Ng’ombe zazing’ono zamphongo zochuluka zandizungulira.+Nkhunzi zamphamvu za ku Basana zandizinga.+
13 Iwo anditsegulira pakamwa pawo mondiopseza,+Ngati mkango wokhadzula nyama umenenso ukubangula.+
14 Ndathiridwa pansi ngati madzi.+Mafupa anga onse alekanalekana.+Mtima wanga wakhala ngati phula,+Wasungunuka mkati mwanga.+
15 Mphamvu yanga yauma gwaa, ngati phale.+Lilime langa lamamatira kunkhama zanga,+Ndipo mwandikhazika m’fumbi la imfa.+
16 Agalu andizungulira.+Khamu la anthu ochita zoipa landizinga.+Iwo akuluma manja ndi mapazi anga ngati mkango.+
17 Ndingathe kuwerenga mafupa anga onse.+Adaniwo akuona zimenezi, ndipo akundiyang’anitsitsa.+
18 Iwo akugawana zovala zanga pakati pawo,+Ndipo akuchita maere pazovala zanga.+
19 Koma inu Yehova, musakhale kutali ndi ine,+Inu mphamvu yanga,+ ndithandizeni mofulumira.+
20 Landitsani moyo wanga ku lupanga,+Moyo wanga wokhawu umene ndili nawo muulanditse m’kamwa mwa galu.+
21 Ndipulumutseni m’kamwa mwa mkango,+Ndipo mundiyankhe ndi kundipulumutsa ku nyanga za ng’ombe zamphongo zam’tchire.+
22 Ndidzalengeza dzina lanu+ kwa abale anga.+Ndidzakutamandani pakati pa mpingo.+
23 Inu oopa Yehova, m’tamandeni!+Inu nonse mbewu ya Yakobo, m’patseni ulemerero!+Ndipo muopeni, inu nonse mbewu ya Isiraeli.+
24 Pakuti iye sananyoze,+Kapena kunyansidwa ndi nsautso ya munthu wosautsidwa.+Ndipo sanam’bisire nkhope yake.+Pamene anamulirira kuti amuthandize, iye anamva.+
25 Chifukwa cha zimene mwachita ndidzakutamandani mumpingo waukulu.+Ndidzakwaniritsa malonjezo anga pamaso pa anthu oopa iye.+
26 Ofatsa adzadya ndi kukhuta.+Ofunafuna Yehova adzamutamanda.+Mitima yanu ikhale ndi moyo kosatha.+
27 Anthu onse okhala kumalekezero a dziko lapansi adzakumbukira Yehova ndi kubwerera kwa iye.+Ndipo mafuko onse a anthu a mitundu ina adzagwada pamaso panu.+
28 Pakuti Yehova ndiye mfumu,+Ndipo akulamulira mitundu.+
29 Anthu onse a padziko lapansi onyada chifukwa cha chuma chawo adzadya ndi kuwerama.+Onse otsikira kufumbi adzawerama pamaso pake,+Ndipo palibe amene adzapulumutsa moyo wake.+
30 Mbewu idzamutumikira.+Adzalengeza za Yehova ku m’badwo wotsatira.+
31 Adzafika ndi kunena za chilungamo chake,+Adzauza anthu amene adzabadwe kuti iye ndiye wachita zimenezi.+