Salimo 101:1-8
Nyimbo ndi Salimo la Davide.
101 Ndidzaimba za kukoma mtima kwanu kosatha ndi chiweruzo chanu.+Inu Yehova, ndidzakuimbirani nyimbo zokutamandani.+
2 Ndidzachita zinthu mwanzeru m’njira yowongoka.+Kodi inu mudzandithandiza liti?+Ndidzayendayenda m’nyumba yanga ndi mtima wanga wosagawanika.+
3 Sindidzaika maso anga pa chinthu chilichonse chopanda pake.+Ndimadana ndi zochita za opatuka pa choonadi.+Sindilola kuti zochita zawozo zindikhudze.+
4 Aliyense wopotoka maganizo amachoka pamaso panga.+Sindichita choipa chilichonse.+
5 Aliyense wonenera mnzake miseche,+Ndimamukhalitsa chete.+Sindingathe kupirira zochita za+Aliyense wodzikweza ndi wamtima wonyada.+
6 Maso anga ali pa okhulupirika a padziko lapansi,+Kuti akhale ndi ine.+Woyenda m’njira yowongoka,+Ndi amene adzanditumikira.+
7 M’nyumba yanga simudzakhala wochita chinyengo.+Ndipo aliyense wolankhula zachinyengo sadzapitiriza kukhala+Pamaso panga.+
8 M’mawa uliwonse ndidzawononga oipa onse a padziko lapansi.+Ndidzapha ndi kuchotsa mumzinda wa Yehova anthu onse ochita zinthu zopweteka anzawo.+