Salimo 36:1-12

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova. 36  Uchimo ukulankhula mumtima mwa munthu woipa.+Maso ake saona chifukwa choopera Mulungu.+   Pakuti amadzinyenga yekha,+Ndipo sazindikira cholakwa chake ndi kudana nacho.+   Mawu a pakamwa pake ndi opweteka ndi achinyengo.+Wasiya kugwiritsa ntchito nzeru zomuthandiza kuchita zinthu zabwino.+   Ali pabedi lake amakonza chiwembu kuti apweteke anzake.+Amaima panjira yoipa.+Sapewa kuchita zinthu zoipa.+   Inu Yehova, kukoma mtima kwanu kosatha kuli kumwamba.+Kukhulupirika kwanu kwafika m’mitambo.+   Inu Mulungu, chilungamo chanu chili ngati mapiri anu.+Chiweruzo chanu ndi chozama kwambiri ngati madzi akuya.+Inu Yehova, mumapulumutsa munthu ndiponso nyama.+   Inu Mulungu, kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwamtengo wapatali!+Ndipo ana a anthu amabisala mu mthunzi wa mapiko anu.+   Amadya ndi kukhuta chakudya chonona m’nyumba mwanu.+Ndipo mumawamwetsa mumtsinje wa zosangalatsa zanu zambiri.+   Pakuti inu ndinu kasupe wa moyo.+Chifukwa cha kuwala kochokera kwa inu, tikuona kuwala.+ 10  Pitirizani kusonyeza kukoma mtima kwanu kosatha kwa anthu okudziwani,+Ndiponso chilungamo chanu kwa anthu owongoka mtima.+ 11  Musalole kuti phazi la anthu odzikweza lindipondereze.+Ndipo musalole dzanja la anthu oipa kundipitikitsa kuti ndikhale wothawathawa.+ 12  Onani, ochita zinthu zopweteka anzawo agwa.+Awakanikizira pansi ndipo sakuthanso kudzuka.+

Mawu a M'munsi