Salimo 46:1-11
Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la ana a Kora+ mogwirizana ndi kaimbidwe ka Atsikana.
46 Mulungu ndiye pothawira pathu ndi mphamvu yathu,+Thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya masautso.+
2 N’chifukwa chake sitidzaopa, ngakhale dziko lapansi litasintha,+Ndiponso ngakhale mapiri atagwedezeka ndi kumira m’nyanja yaikulu.+
3 Ngakhale madzi a m’nyanjayo atawinduka ndi kuchita thovu,+Ndiponso ngakhale mapiri atagwedezeka chifukwa cha phokoso la nyanja yaikuluyo.+ [Seʹlah.]
4 Pali mtsinje womwe nthambi zake zimachititsa anthu a mumzinda wa Mulungu kukondwera,+Chihema chachikulu chopatulika koposa cha Wam’mwambamwamba.+
5 Mulungu ali pakati pa mzinda.+ Mzindawo sudzagwedezeka.+Mulungu adzauthandiza m’bandakucha.+
6 Mitundu ya anthu inachita phokoso,+ maufumu anagwedezeka.Iye anatulutsa mawu ndipo dziko lapansi linasungunuka.+
7 Yehova wa makamu ali ndi ife.+Mulungu wa Yakobo ndiye malo athu okwezeka ndiponso achitetezo.+ [Seʹlah.]
8 Bwerani anthu inu, onani ntchito za Yehova,+Onani mmene wakhazikitsira zinthu zodabwitsa padziko lapansi.+
9 Akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+Wathyola uta ndi kuduladula mkondo.+Ndipo watentha magaleta pamoto.+
10 “Gonjerani anthu inu, ndipo dziwani kuti ine ndine Mulungu.+Ndidzakwezedwa pakati pa anthu a mitundu ina,+Ndidzakwezedwa padziko lapansi.”+
11 Yehova wa makamu ali ndi ife.+Mulungu wa Yakobo ndiye malo athu okwezeka ndiponso achitetezo.+ [Seʹlah.]