Salimo 100:1-5
Nyimbo yoyamikira.+
100 Fuulirani Yehova mosangalala inu nonse anthu a padziko lapansi chifukwa wapambana.+
2 Tumikirani Yehova mokondwera.+Bwerani kwa iye mukufuula mosangalala.+
3 Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu.+Iye ndi amene anatipanga, sitinadzipange tokha.+Ndife anthu ake ndi nkhosa zimene akuweta.+
4 Lowani pazipata zake ndi mawu oyamikira,+Lowani m’mabwalo ake ndi mawu otamanda.+Muyamikeni, tamandani dzina lake.+
5 Pakuti Yehova ndi wabwino.+Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapo mpaka kalekale,+Ndipo kukhulupirika kwake kudzakhalapo ku mibadwomibadwo.+