Salimo 85:1-13

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora. 85  Inu Yehova, mwasangalala ndi dziko lanu.+Mwabwezeretsa ana a Yakobo amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina.+   Mwakhululukira anthu anu zolakwa zawo.+Mwaphimba machimo awo onse.+ [Seʹlah.]   Mwalamulira mkwiyo wanu wonse,+Ndipo simunasonyeze kutentha kwa mkwiyo wanu.+   Tisonkhanitseni ndi kutibwezeretsa mwakale, inu Mulungu wa chipulumutso chathu,+Ndipo tichotsereni mkwiyo wanu.+   Kodi mupitiriza kutikwiyira mpaka kalekale?+Kodi mudzasonyeza mkwiyo wanu ku mibadwomibadwo?+   Kodi simutitsitsimutsanso+Kuti anthu anu akondwere chifukwa cha inu?+   Inu Yehova, tisonyezeni kukoma mtima kwanu kosatha,+Ndipo tipatseni chipulumutso chanu.+   Ndidzamvetsera zimene Mulungu woona Yehova adzanena,+Pakuti adzanena za mtendere kwa anthu ake+ ndi kwa okhulupirika ake.Koma iwo asadzidalire kwambiri ngati kale.+   Ndithudi, chipulumutso chake chili pafupi ndi amene amamuopa,+Kuti ulemerero ukhale m’dziko lathu.+ 10  Kukoma mtima kosatha ndi choonadi zakumana.+Chilungamo ndi mtendere zapsompsonana.+ 11  Choonadi chidzaphuka padziko lapansi,+Ndipo chilungamo chidzayang’ana pansi kuchokera kumwamba.+ 12  Yehova nayenso adzapereka zinthu zabwino,+Ndipo dziko lathu lidzapereka zipatso zake.+ 13  Chilungamo chidzayenda pamaso pake,+Ndipo chidzapanga njira yotsatira mapazi a Mulungu.+

Mawu a M'munsi