Salimo 138:1-8

Salimo la Davide. 138  Ndidzakutamandani ndi mtima wanga wonse.+Ndidzakuimbirani nyimbo zokutamandani pamaso pa milungu ina.+   Ndidzawerama nditayang’ana kukachisi wanu woyera,+Ndipo ndidzatamanda dzina lanu+Chifukwa cha kukoma mtima kwanu kosatha+ ndi choonadi chanu.+Pakuti malonjezo+ amene munawachita m’dzina lanu ndi aakulu ndithu. Koma kukwaniritsidwa kwa malonjezowo n’kwakukulu koposa.+   Pa tsiku limene ine ndinaitana, inu munandiyankha.+Munandilimbitsa mtima ndi kundipatsa mphamvu.+   Mafumu onse a padziko lapansi adzakutamandani, inu Yehova,+Pakuti adzakhala atamva mawu a pakamwa panu.   Ndipo iwo adzaimba za njira za Yehova,+Pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.+   Ngakhale kuti Yehova ali pamwamba, amaona wodzichepetsa,+Koma wodzikuza samuyandikira.+   Ndikakhala pa masautso, inu mudzandisunga wamoyo.+Mudzatambasula dzanja lanu chifukwa cha mkwiyo wa adani anga,+Ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.+   Yehova adzakwaniritsa zolinga zimene ali nazo pa ine.+Inu Yehova, kukoma mtima kwanu kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+Musasiye ntchito ya manja anu.+

Mawu a M'munsi