Salimo 119:1-176
א [ʼAʹleph]
119 Odala ndi anthu osalakwitsa kanthu m’njira zawo,+Anthu amene akutsatira chilamulo cha Yehova.+
2 Odala ndi anthu amene amasunga zikumbutso zake,+Amene amayesetsa kumufunafuna ndi mtima wonse.+
3 Ndithu, iwo sachita chinthu chosalungama.+Amayenda m’njira zake.+
4 Inu mwatilamula kuti tisunge+Malamulo anu mosamala.+
5 Haa! Ndikanakonda kuti ndiyende mowongoka+Kuti ndisunge malangizo anu,+
6 Pamenepo sindikanachita manyazi,+Pamene ndikulabadira malamulo anu onse.+
7 Ndidzakutamandani ndi mtima wowongoka,+Pamene ndikuphunzira zigamulo zanu zolungama.+
8 Ndikupitiriza kusunga malangizo anu,+Choncho musandisiyiretu.+
ב [Behth]
9 Kodi wachinyamata+ angakhale bwanji woyera pa moyo wake?Mwa kudziyang’anira ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi mawu anu.+
10 Ndayesetsa kukufunafunani ndi mtima wanga wonse.+Musandichititse kusochera ndi kuchoka pa malamulo anu.+
11 Ndasunga mosamala mawu anu mumtima mwanga,+Kuti ndisakuchimwireni.+
12 Ndinu wodala inu Yehova.Ndiphunzitseni malamulo anu.+
13 Ndi milomo yanga ndalengeza+Zigamulo zonse zotuluka pakamwa panu.+
14 Ndimakondwera kuyenda m’njira ya zikumbutso zanu,+Ngati mmene anthu amachitira akapeza chuma chilichonse chamtengo wapatali.+
15 Ndidzasinkhasinkha malamulo anu,+Ndipo ndidzalabadira njira zanu.+
16 Ndidzakonda malamulo anu.+Ndipo sindidzaiwala mawu anu.+
ג [Giʹmel]
17 Ndichitireni zabwino, ine mtumiki wanu, kuti ndikhale ndi moyo,+Ndi kuti ndisunge mawu anu.+
18 Tsegulani maso anga kuti ndione+Zinthu zodabwitsa za m’chilamulo chanu.+
19 Ine ndine mlendo m’dziko ili.+Musandibisire malamulo anu.+
20 Moyo wanga wasautsika chifukwa cholakalaka+Zigamulo zanu nthawi zonse.+
21 Mwadzudzula odzikuza otembereredwa,+Amene akusochera ndi kuchoka pa malamulo anu.+
22 Mugubuduze ndi kuchotsa chitonzo ndi kunyozedwa kwanga,+Pakuti ndasunga zikumbutso zanu.+
23 Akalonga asonkhana pamodzi kuti akambirane zondiukira.+Koma ine mtumiki wanu, ndimasinkhasinkha malangizo anu.+
24 Ndimakonda zikumbutso zanu,+Ndipo zili ngati anthu amene amandipatsa malangizo.+
ד [Daʹleth]
25 Moyo wanga wamamatira kufumbi.+Ndisungeni wamoyo mogwirizana ndi mawu anu.+
26 Ndakuuzani za njira zanga kuti mundiyankhe.+Ndiphunzitseni malamulo anu.+
27 Ndithandizeni kumvetsa njira zofotokozedwa m’malamulo anu,+Kuti ndisinkhesinkhe ntchito zanu zodabwitsa.+
28 Ine ndikusowa tulo chifukwa cha chisoni.+Ndilimbitseni ndi mawu anu.+
29 Ndichotsereni njira yolakwika,+Ndikomereni mtima mwa kundipatsa chilamulo chanu.+
30 Ine ndasankha kuyenda mokhulupirika.+Zigamulo zanu ndimaziona kukhala zoyenera.+
31 Ndamamatira zikumbutso zanu.+Inu Yehova, musandichititse manyazi.+
32 Ndidzamvera malamulo anu,+Chifukwa mwandichititsa kuwamvetsa bwino.+
ה [Heʼ]
33 Ndilangizeni inu Yehova, kuti ndiyende motsatira malangizo anu,+Kuti nditsatire malangizo anu moyo wanga wonse.+
34 Ndithandizeni kukhala wozindikira kuti nditsatire chilamulo chanu,+Ndiponso kuti ndichisunge ndi mtima wonse.+
35 Ndiyendetseni m’njira ya malamulo anu,+Pakuti ndikukondwera ndi njira imeneyi.+
36 Ndithandizeni kuti mtima wanga uziganizira zikumbutso zanu,+Osati kupeza phindu.*+
37 Chititsani maso anga kuti asaone zinthu zopanda pake.+Ndiyendetseni m’njira yanu kuti ndikhalebe wamoyo.+
38 Kwaniritsani mawu anu pa mtumiki wanu,+Mawu amene amachititsa mtumiki wanu kukuopani.+
39 Ndichotsereni chitonzo chimene ndikuchiopa,+Pakuti zigamulo zanu ndi zabwino.+
40 Taonani! Ine ndikulakalaka malamulo anu.+Ndisungeni wamoyo mogwirizana ndi chilungamo chanu.+
ו [Waw]
41 Monga mwa mawu anu, inu Yehova, ndipatseni chipulumutso chanu.+Ndipatseni zochita zanu zosonyeza kukoma mtima kosatha,+
42 Kuti ndipeze choyankha kwa wonditonza,+Pakuti ine ndakhulupirira mawu anu.+
43 Musachotse mawu a choonadi pakamwa panga,+Pakuti ndayembekezera chigamulo chanu.+
44 Ndidzasunga chilamulo chanu nthawi zonse,+Mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+
45 Ndidzayenda uku ndi uku m’malo otakasuka,+Chifukwa ndaphunzira malamulo anu ndi kuwasunga.+
46 Komanso ndidzanena za zikumbutso zanu pamaso pa mafumu,+Ndipo sindidzachita manyazi.+
47 Ndidzakondwera ndi malamulo anu+Amene ndimawakonda.+
48 Ndidzapemphera kwa inu nditakweza manja anga chifukwa ndimakonda malamulo anu,+Ndipo ndidzasinkhasinkha malangizo anu.+
ז [Zaʹyin]
49 Kumbukirani mawu amene munandiuza ine mtumiki wanu,+Mawu amene ndikuwayembekezera malinga ndi lonjezo lanu.+
50 Chimenechi ndi chilimbikitso changa mu nsautso yanga,+Pakuti mawu anu andisungabe wamoyo.+
51 Anthu odzikuza andinyoza koopsa.+Koma ine sindinapatuke pa chilamulo chanu.+
52 Ndimakumbukira zigamulo zanu zakalekale inu Yehova,+Ndipo zimandilimbikitsa.+
53 Mkwiyo ukuyaka mumtima mwanga chifukwa cha oipa,+Amene akusiya chilamulo chanu.+
54 Kwa ine, malangizo anu akhala ngati nyimbo zokutamandani,+M’nyumba zimene ndimakhala m’mayiko achilendo.+
55 Usiku ndimakumbukira dzina lanu, inu Yehova,+Kuti ndisunge chilamulo chanu.+
56 Ndi zimenetu zandichitikira ine,Chifukwa ndimatsatira malamulo anu.+
ח [Chehth]
57 Yehova, inu ndiye cholowa changa.+Ndalonjeza kusunga mawu anu.+
58 Ndayesetsa ndi mtima wanga wonse kuti mundiyanje.*+Ndikomereni mtima monga mwa mawu anu.+
59 Ndaganizira mozama za njira zanga,+Kuti mapazi anga ndiwabwezere ku zikumbutso zanu.+
60 Ndinafulumira ndipo sindinazengereze+Kusunga malamulo anu.+
61 Zingwe za oipa zinandikulunga,+Koma ine sindinaiwale chilamulo chanu.+
62 Pakati pa usiku ndimadzuka kuti ndikuyamikeni+Chifukwa cha zigamulo zanu zolungama.+
63 Ine ndine mnzawo wa anthu okuopani,+Ndiponso wa anthu osunga malamulo anu.+
64 Inu Yehova, kukoma mtima kwanu kosatha kwadzaza dziko lonse lapansi.+Ndiphunzitseni malamulo anu.+
ט [Tehth]
65 Inu Yehova, mwandichitiradi zabwino ine mtumiki wanu,+Monga mwa mawu anu.+
66 Ndiphunzitseni kuchita zabwino,+ kulingalira bwino+ ndi kudziwa zinthu,+Pakuti ndimakhulupirira malamulo anu.+
67 Ndisanagwe m’masautso ndinali kuchimwa mosadziwa,+Koma tsopano ndimasunga mawu anu.+
68 Inu ndinu wabwino ndipo mukuchita zabwino.+Ndiphunzitseni malamulo anu.+
69 Anthu odzikuza andinenera mabodza ambiri,+Koma ine ndidzasunga malamulo anu ndi mtima wanga wonse.+
70 Mitima yawo yauma ngati mafuta oundana,+Koma ine ndimakonda chilamulo chanu.+
71 Zili bwino kuti ndasautsika,+Kuti ndiphunzire malamulo anu.+
72 Chilamulo+ chotuluka pakamwa panu n’chabwino kwa ine,+N’chabwino kwambiri kuposa ndalama masauzande zagolide ndi zasiliva.+
י [Yohdh]
73 Manja anu anandipanga, ndipo anandiumba.+Ndithandizeni kukhala wozindikira, kuti ndiphunzire malamulo anu.+
74 Oopa inu ndi amene amasangalala akandiona,+Chifukwa ndayembekezera mawu anu.+
75 Inu Yehova, ndikudziwa bwino kuti zigamulo zanu ndi zolungama,+Ndiponso kuti mwandilanga chifukwa chakuti ndinu wokhulupirika.+
76 Kukoma mtima kwanu kosatha kundilimbikitse,+Monga mwa mawu anu kwa ine mtumiki wanu.+
77 Ndisonyezeni chifundo chanu kuti ndikhalebe ndi moyo,+Pakuti ndimakonda chilamulo chanu.+
78 Odzikuza achite manyazi, chifukwa andisocheretsa popanda chifukwa,+Koma ine ndimasinkhasinkha malamulo anu.+
79 Anthu okuopani abwerere kwa ine,+Chimodzimodzinso odziwa zikumbutso zanu.+
80 Mtima wanga usunge malangizo anu mosalakwitsa kanthu,+Kuti ndisachite manyazi.+
כ [Kaph]
81 Ine ndafooka chifukwa cholakalaka chipulumutso chanu,+Pakuti ndayembekezera mawu anu.+
82 Maso anga alefuka chifukwa cholakalaka mawu anu,+Ndipo ndikunena kuti: “Kodi mudzandilimbikitsa liti?”+
83 Ndakhala ngati thumba lachikopa+ mu utsi,Koma sindinaiwale malangizo anu.+
84 Kodi ine mtumiki wanu ndidikira kufikira liti?+Kodi anthu ondizunza mudzawaweruza liti?+
85 Anthu amene sachita zinthu mogwirizana ndi chilamulo chanu,+Anthu odzikuza akumba mbuna kuti andigwire.+
86 Malamulo anu onse ndi odalirika.+Odzikuza andizunza popanda chifukwa. Chonde, ndithandizeni.+
87 Iwo anangotsala pang’ono kundifafaniza padziko lapansi,+Koma ine sindinasiye malamulo anu.+
88 Ndisungeni wamoyo monga mwa kukoma mtima kwanu kosatha,+Kuti ndisunge zikumbutso zotuluka pakamwa panu.+
ל [Laʹmedh]
89 Inu Yehova, mawu anu anakhazikika kumwamba,+Mpaka kalekale.+
90 Kukhulupirika kwanu kudzakhalapobe ku mibadwomibadwo.+Mwakhazikitsa mwamphamvu dziko lapansi, kuti lisagwedezeke.+
91 Chilengedwe chonse chakhalapobe kufikira lero chifukwa cha zigamulo zanu,+Pakuti chilengedwe chonse chimakutumikirani.+
92 Ndikanapanda kukonda chilamulo chanu,+Ndikanatheratu m’masautso anga.+
93 Sindidzaiwala malamulo anu mpaka kalekale,+Chifukwa mwandisungabe wamoyo kudzera m’malamulo amenewo.+
94 Ine ndine wanu. Chonde ndipulumutseni,+Chifukwa ndaphunzira malamulo anu ndi kuwasunga.+
95 Oipa amandiyembekezera kuti andiwononge,+Koma ine ndimamvetsera zikumbutso zanu.+
96 Ndaona kuti zinthu zonse zabwino kwambiri zili ndi malire.+Koma malamulo anu amakhudza mbali zonse.
מ [Mem]
97 Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu!+Ndimasinkhasinkha chilamulocho tsiku lonse.+
98 Malamulo anu amandichititsa kukhala wanzeru kuposa adani anga,+Chifukwa ndi anga mpaka kalekale.+
99 Ndakhala wozindikira kwambiri kuposa aphunzitsi anga,+Chifukwa ndimasinkhasinkha zikumbutso zanu.+
100 Ndimachita zinthu mozindikira kuposa anthu achikulire,+Chifukwa ndimasunga malamulo anu.+
101 Ndaletsa mapazi anga kuyenda m’njira iliyonse yoipa.+Ndachita izi kuti ndisunge mawu anu.+
102 Sindinapatuke pa zigamulo zanu,+Pakuti inu mwandilangiza.+
103 Mawu anu amatsekemera m’kamwa mwanga,Kuposa mmene uchi umakomera!+
104 Chifukwa cha malamulo anu ndimachita zinthu mozindikira.+N’chifukwa chake ndimadana ndi njira iliyonse yachinyengo.+
נ [Nun]
105 Mawu anu ndi nyale younikira kumapazi anga,+Ndi kuwala kounikira njira yanga.+
106 Ndalumbira kuti ndidzasunga zigamulo zanu zolungama,+Ndipo ndidzakwaniritsa lumbiro langa.+
107 Ndasautsika kwambiri.+Inu Yehova, ndisungenibe wamoyo monga mwa mawu anu.+
108 Inu Yehova, chonde kondwerani ndi nsembe zaufulu za pakamwa panga,+Ndipo ndiphunzitseni zigamulo zanu.+
109 Moyo wanga uli pangozi nthawi zonse,*+Koma sindinaiwale chilamulo chanu.+
110 Oipa anditchera msampha,+Koma ine sindinasochere ndi kuchoka pa malamulo anu.+
111 Ndatenga zikumbutso zanu kukhala chuma changa mpaka kalekale,+Pakuti zimakondweretsa mtima wanga.+
112 Ndatsimikiza mtima kutsatira malangizo anu,+Mpaka kalekale, ndithu kwa moyo wanga wonse.+
ס [Saʹmekh]
113 Ndimadana ndi anthu amitima iwiri,+Koma ndimakonda chilamulo chanu.+
114 Inu ndinu malo anga obisalamo ndi chishango changa,+Pakuti ndayembekezera mawu anu.+
115 Ndichokereni anthu ochita zoipa inu,+Kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga.+
116 Inu Mulungu, ndithandizeni monga mwa mawu anu kuti ndikhalebe ndi moyo,+Ndipo musandichititse manyazi chifukwa cha chiyembekezo changa.+
117 Ndithandizeni kuti ndipulumutsidwe,+Ndipo ndidzamvera malangizo anu nthawi zonse.+
118 Onse osochera ndi kuchoka pa malangizo anu mwawataya kutali,+Pakuti ndi achinyengo komanso onama.+
119 Anthu onse oipa mwawachotsa padziko lapansi ngati zonyansa.*+N’chifukwa chake ine ndimakonda zikumbutso zanu.+
120 Chifukwa choopa inu, thupi langa linagwidwa nthumanzi,+Ndipo chifukwa cha zigamulo zanu, ndinachita mantha.+
ע [ʽAʹyin]
121 Ndapereka ziweruzo zolungama ndipo ndachita zinthu mwachilungamo.+Musandipereke kwa anthu ondichitira chinyengo.+
122 Khalani ngati chikole kwa ine mtumiki wanu kuti mudzandichitira zabwino.+Anthu odzikuza asandichitire chinyengo.+
123 Maso anga afooka chifukwa cholakalaka chipulumutso chanu+Ndi mawu anu olungama.+
124 Ndichitireni zabwino ine mtumiki wanu monga mwa kukoma mtima kwanu kosatha,+Ndipo ndiphunzitseni malamulo anu.+
125 Ine ndine mtumiki wanu.+ Ndithandizeni kukhala wozindikira,+Kuti ndidziwe zikumbutso zanu.+
126 Ino ndi nthawi yakuti inu Yehova muchitepo kanthu,+Chifukwa anthu odzikuzawo aphwanya chilamulo chanu.+
127 N’chifukwa chake ine ndimakonda malamulo anu+Kuposa golide, golide woyenga bwino.+
128 Choncho ndaona kuti malamulo anu onse okhudza chilichonse ndi olungama.+Ndimadana ndi njira iliyonse yachinyengo.+
פ [Peʼ]
129 Zikumbutso zanu n’zodabwitsa.+N’chifukwa chake ine ndimazisunga.+
130 Kuululidwa kwa mawu anu kumapereka kuwala,+Kumathandiza anthu osadziwa zambiri kukhala ozindikira.+
131 Ndatsegula kwambiri pakamwa panga kuti ndipume mofulumira,+Chifukwa ndikulakalaka malamulo anu.+
132 Ndicheukireni ndi kundikomera mtima,+Mogwirizana ndi zigamulo zimene mumapereka kwa anthu okonda dzina lanu.+
133 Mwapondetsa mwamphamvu mapazi anga pa mawu anu,+Ndipo musalole kuti choipa chilichonse chindilamulire.+
134 Ndiwomboleni kwa munthu aliyense wondichitira zachinyengo,+Ndipo ine ndidzasunga malamulo anu.+
135 Ndikomereni mtima ine mtumiki wanu,+Ndipo ndiphunzitseni malamulo anu.+
136 Misozi yatsika m’maso mwanga ngati mitsinje ya madzi,+Chifukwa chakuti iwo sanasunge chilamulo chanu.+
צ [Tsa·dhehʹ]
137 Ndinu wolungama inu Yehova,+Ndipo zigamulo zanu ndi zowongoka.+
138 M’chilungamo chanu ndiponso kukhulupirika kwanu kosaneneka+Mwatilamula kuti tisunge zikumbutso zanu.+
139 Changu changa chandidya,+Chifukwa adani anga aiwala mawu anu.+
140 Mawu anu ndi oyengeka kwambiri,+Ndipo ine mtumiki wanu ndimawakonda.+
141 Kwa ena ndine wopanda pake ndi wonyozeka.+Koma sindinaiwale malamulo anu.+
142 Chilungamo chanu ndi chilungamo mpaka kalekale,+Ndipo chilamulo chanu ndi choonadi.+
143 Zowawa ndi zovuta zinandigwera.+Koma ndinakonda malamulo anu.+
144 Zikumbutso zanu zidzakhalabe zolungama mpaka kalekale.+Ndithandizeni kukhala wozindikira kuti ndikhalebe ndi moyo.+
ק [Qohph]
145 Ndaitana ndi mtima wanga wonse.+ Ndiyankheni inu Yehova.+Ndidzasunga malangizo anu.+
146 Ndakuitanani. Ndipulumutseni chonde!+Ndidzasunga zikumbutso zanu.+
147 Ndadzuka m’mawa kuli mbuu,+ kuti ndipemphe thandizo kwa inu,+Pakuti ndayembekezera mawu anu.+
148 Ndimadzuka pa ulonda wa usiku,+Kuti ndisinkhesinkhe mawu anu.+
149 Imvani mawu anga mwa kukoma mtima kwanu kosatha.+Inu Yehova, ndisungenibe wamoyo mogwirizana ndi zigamulo zanu.+
150 Okonda kuchita khalidwe lotayirira+ abwera pafupi ndi ine.Iwo atalikirana kwambiri ndi chilamulo chanu.+
151 Inu Yehova muli pafupi,+Ndipo malamulo anu onse ndi choonadi.+
152 Zina mwa zikumbutso zanu ndinazidziwa kale kwambiri,+Pakuti munazikhazikitsa kalekale.+
ר [Rehsh]
153 Onani kusautsika kwanga ndipo ndipulumutseni,+Pakuti sindinaiwale chilamulo chanu.+
154 Ndiyankhireni mlandu wanga ndi kundipulumutsa.+Ndisungeni wamoyo mogwirizana ndi mawu anu.+
155 Chipulumutso chili kutali ndi anthu oipa,+Pakuti sanaphunzire malamulo anu ndi kuwasunga.+
156 Chifundo chanu n’chachikulu, inu Yehova.+Ndisungenibe wamoyo mogwirizana ndi zigamulo zanu.+
157 Anthu ondizunza komanso adani anga ndi ambiri.+Koma ine sindinapatuke pa zikumbutso zanu.+
158 Ndaona anthu ochita zinthu mwachinyengo,+Ndipo amandinyansa chifukwa sasunga mawu anu.+
159 Onani kuti ndimakonda malamulo anu.+Inu Yehova, ndisungenibe wamoyo mwa kukoma mtima kwanu kosatha.+
160 Mawu anu onse ndi choonadi chokhachokha,+Ndipo chigamulo chanu chilichonse cholungama chidzakhalapo mpaka kalekale.+
ש [Sin] kapena kuti [Shin]
161 Akalonga andizunza popanda chifukwa,+Koma mtima wanga umaopa mawu anu.+
162 Ndikukondwera chifukwa cha mawu anu,+Monga mmene munthu amachitira akapeza zofunkha zambiri.+
163 Ndimadana ndi chinyengo+ ndipo chimandinyansa,+Koma ndimakonda chilamulo chanu.+
164 Ndimakutamandani maulendo 7 pa tsiku,+Chifukwa cha zigamulo zanu zolungama.+
165 Okonda chilamulo chanu amapeza mtendere wochuluka,+Ndipo palibe chowakhumudwitsa.+
166 Ndayembekezera chipulumutso chanu, inu Yehova,+Ndipo ndatsatira malamulo anu.+
167 Ndasunga zikumbutso zanu,+Ndipo ndimazikonda kwambiri.+
168 Ndasunga malamulo anu ndi zikumbutso zanu,+Pakuti njira zanga zonse zili pamaso panu.+
ת [Taw]
169 Inu Yehova, imvani kulira kwanga kochonderera.+Ndithandizeni kuti ndikhale wozindikira, monga mwa mawu anu.+
170 Pempho langa lakuti mundichitire chifundo lifike kwa inu.+Ndipulumutseni monga mwa mawu anu.+
171 Milomo yanga itulutse mawu okutamandani,+Pakuti mwandiphunzitsa malamulo anu.+
172 Lilime langa liimbe za mawu anu,+Pakuti malamulo anu onse ndi olungama.+
173 Dzanja lanu lindithandize,+Chifukwa ndasankha malamulo anu.+
174 Ndikulakalaka chipulumutso chanu, inu Yehova,+Ndipo ndimakonda kwambiri chilamulo chanu.+
175 Ndisungenibe wamoyo kuti ndikutamandeni,+Zigamulo zanu zindithandize.+
176 Ndayendayenda ngati nkhosa yosochera.+ Ndifunefuneni ine mtumiki wanu,+Pakuti sindinaiwale malamulo anu.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti “phindu lopezeka mwachinyengo pamalonda.”
^ Mawu ake enieni, “ndafewetsa nkhope yanu.”
^ Mawu ake enieni, “moyo wanga uli m’dzanja langa.”
^ Zimenezi ndi zonyansa zotsalira poyenga zitsulo.