Salimo 107:1-43
(Masalimo 107 – 150)
107 Yamikani Yehova anthu inu, pakuti iye ndi wabwino.+Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
2 Anthu owomboledwa a Yehova anene zimenezi,+Anthu amene iye wawawombola m’manja mwa mdani,+
3 Anthu amene anawasonkhanitsa pamodzi kuchokera m’mayiko osiyanasiyana,+Kuchokera kotulukira dzuwa kukafika kolowera dzuwa,+Kuchokera kumpoto kukafika kum’mwera.+
4 Iwo anayendayenda m’chipululu+ mopanda kanthu.+Sanapeze njira iliyonse yopita kumzinda woti azikhalamo.+
5 Anali ndi njala komanso ludzu.+Anafooka kwambiri, kutsala pang’ono kufa.+
6 Iwo anapitiriza kufuulira Yehova m’masautso awo,+Ndipo anawalanditsa ku mavuto awo.+
7 Anawayendetsa m’njira yabwino,+Kuti akafike kumzinda woti azikhalamo.+
8 Anthu ayamike Yehova chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha,+Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+
9 Pakuti iye wapereka madzi kwa anthu aludzu.+Ndipo anthu anjala wawadyetsa zinthu zabwino.+
10 Ena anali kukhala mu mdima, mu mdima wandiweyani,+Anali akaidi osautsika ndi omangidwa maunyolo,+
11 Chifukwa anachita zinthu mopandukira+ mawu a Mulungu,+Ndipo ananyoza malangizo a Wam’mwambamwamba.+
12 Choncho mwa kuwadzetsera mavuto, Mulungu anagonjetsa mitima yawo.+Iwo anapunthwa ndipo panalibe wowathandiza.+
13 Iwo anayamba kuitana Yehova kuti awathandize m’masautso awo,+Ndipo iye anawapulumutsa ku mavuto awo monga mwa nthawi zonse.+
14 Iye anawatulutsa mu mdima, mu mdima wandiweyani,+Ndi kudula zingwe zimene anamangidwa nazo.+
15 Anthu ayamike Yehova chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha,+Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+
16 Pakuti iye wathyola zitseko zamkuwa,+Ndipo wadula mipiringidzo yachitsulo.+
17 Anthu amene anali opusa chifukwa cha njira yawo yophwanya malamulo,+Komanso chifukwa cha zolakwa zawo, pamapeto pake anadzibweretsera masautso.+
18 Moyo wawo unaipidwa ndi chakudya cha mtundu uliwonse,+Ndipo anafika pazipata za imfa.+
19 Iwo anayamba kuitana Yehova kuti awathandize m’masautso awo.+Ndipo iye anawapulumutsa ku mavuto awo monga mwa nthawi zonse.+
20 Iye ananena mawu ndipo anawachiritsa,+Moti anawapulumutsa kudzenje la manda.+
21 Anthu ayamike Yehova chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha,+Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+
22 Iwo apereke nsembe zoyamikira,+Ndi kulengeza za ntchito zake ndi mfuu yachisangalalo.+
23 Anthu amene amayenda m’zombo panyanja,+Amene amachita malonda pamadzi ambiri,+
24 Amenewa ndi amene aona ntchito za Yehova,+Ndiponso ntchito zake zodabwitsa m’madzi akuya.+
25 Aona mmene amautsira mphepo yamkuntho mwa kungonena mawu,+Moti nyanjayo imachita mafunde.+
26 Iwo amapita pamwamba,Kenako amatsika pansi.Chifukwa cha masoka, mitima yawo imasungunuka.+
27 Amadzandira ndipo amayenda peyupeyu ngati munthu woledzera,+Ndipo ngakhale nzeru zawo zonse zimasokonezeka.+
28 Iwo amayamba kufuulira Yehova m’masautso awo,+Ndipo iye amawatulutsa m’mavuto awo.+
29 Iye amachititsa mphepo yamkuntho kukhala bata,+Moti mafunde a panyanja amadekha.+
30 Iwo amasangalala chifukwa mafundewo atha,Ndipo Mulungu amawatsogolera kudoko limene iwo akufuna.+
31 Anthu ayamike Yehova chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha,+Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+
32 Amukweze mumpingo wa anthu,+Ndipo amutamande m’bwalo la anthu achikulire.+
33 Amasandutsa mitsinje kukhala chipululu,+Ndiponso akasupe a madzi kukhala malo opanda madzi.+
34 Nthaka yobala zipatso amaisandutsa dziko lamchere,+Chifukwa cha kuipa kwa anthu okhala mmenemo.
35 Amasandutsa chipululu kukhala dambo la madzi,+Ndipo dziko lopanda madzi amalisintha kukhala dera la akasupe amadzi.+
36 Kumeneko amakhazikako anthu anjala,+Kuti amange mzinda woti azikhalamo.+
37 Anthuwo amafesa mbewu ndi kulima minda ya mpesa,+Kuti akhale ndi zokolola.+
38 Mulungu amawadalitsa moti amachuluka kwambiri,+Ndipo salola kuti ng’ombe zawo zikhale zochepa.+
39 Koma iwo amakhalanso ochepa ndipo amawerama,+Chifukwa cha kuponderezedwa, masoka ndi chisoni.+
40 Mulungu akutsanulira mnyozo pa anthu olemekezeka,+Moti iye akuwachititsa kuyendayenda m’chipululu, mmene mulibe njira.+
41 Koma akuteteza munthu wosauka ku nsautso,+Ndipo akumuchulukitsa kukhala mabanja ambiri ngati gulu la nkhosa.+
42 Olungama amaona ndi kukondwera.+Koma anthu onse osalungama amatseka pakamwa.+
43 Wanzeru ndani? Iye aona zimenezi,+Ndi kuchita chidwi ndi ntchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha.+