Salimo 67:1-7
Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Nyimbo ndi Salimo.
67 Mulungu adzatiyanja ndi kutidalitsa.+Iye adzatikomera mtima,+ [Seʹlah.]
2 Kuti njira zanu zidziwike padziko lapansi,+Kuti chipulumutso chanu chidziwike pakati pa mitundu yonse ya anthu.+
3 Inu Mulungu, mitundu ya anthu ikutamandeni,+Ndithu mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.+
4 Mitundu ya anthu isangalale ndi kufuula mokondwera,+Pakuti inu mudzaweruza anthu molungama.+Ndipo mudzatsogolera mitundu ya anthu padziko lapansi. [Seʹlah.]
5 Inu Mulungu, mitundu ya anthu ikutamandeni,+Ndithu mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.+
6 Dziko lapansi lidzapereka zipatso zake.+Mulungu, ndithu Mulungu wathu, adzatidalitsa.+
7 Mulungu adzatidalitsa,+Ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzamuopa.+