Salimo 8:1-9
Kwa wotsogolera nyimbo pa Gititi.*+ Nyimbo ya Davide.
8 Inu Yehova Ambuye wathu, dzina lanu ndi lalikulu padziko lonse lapansi,+Inuyo ulemerero wanu ukusimbidwa kumwambamwamba!+
2 M’kamwa mwa ana aang’ono ndi ana oyamwa mwakhazikitsamo zamphamvu,+Chifukwa cha amene akukuchitirani zoipa.+Mwatero kuti mugonjetse mdani wanu komanso amene akufuna kukubwezerani zoipa.+
3 Ndikayang’ana kumwamba, ntchito ya zala zanu,+Mwezi ndi nyenyezi zimene munapanga,+
4 Ndimaganiza kuti: Munthu+ ndani kuti muzimuganizira,+Ndipo mwana wa munthu wochokera kufumbi ndani kuti muzimusamalira?+
5 Munamuchepetsa pang’ono poyerekeza ndi ena onga Mulungu,*+Kenako munamuveka ulemerero+ ndi ulemu monga chisoti chachifumu.+
6 Munamupatsa mphamvu kuti alamulire ntchito za manja anu.+Mwaika zonse pansi pa mapazi ake:+
7 Nkhosa, mbuzi ndi ng’ombe zamphongo, zonse zimenezi,+Komanso zilombo zakutchire.+
8 Mbalame zam’mlengalenga ndi nsomba za m’nyanja,+Chilichonse choyenda m’njira za pansi pa nyanja.+
9 Inu Yehova Ambuye wathu, dzina lanu ndi lalikulu padziko lonse lapansi!+
Mawu a M'munsi
^ “Gititi” ndi mawu achiheberi amene anali kuwagwiritsa ntchito polemba nyimbo, koma tanthauzo lake lenileni silikudziwika.
^ Kapena kuti “angelo.”