Salimo 144:1-15

Salimo la Davide. 144  Atamandike Yehova Thanthwe langa,+Amene akuphunzitsa manja anga kumenya nkhondo,+Amenenso akuphunzitsa zala zanga kumenyana ndi adani anga.   Iye amandisonyeza kukoma mtima kwake kosatha ndipo ndiye malo anga achitetezo,+Malo anga okwezeka ndi Wopereka chipulumutso,+Chishango+ changa ndi malo anga othawirako.+Iye amandigonjetsera mitundu ya anthu.+   Inu Yehova, munthu ndani kuti mumuganizire?+Kodi mwana wa munthu wochokera kufumbi+ ndani kuti mumuwerengere?   Munthu amafanana ndi mpweya wotuluka m’mphuno.+Masiku ake ali ngati mthunzi wongodutsa.+   Inu Yehova, weramitsani kumwamba kuti mutsike.+Khudzani mapiri kuti afuke utsi.+   Ng’animitsani mphezi kuti muwabalalitse.+Tumizani mivi yanu kuti muwasokoneze.+   Tambasulani manja anu kuchokera kumwamba.+Ndimasuleni ndi kundilanditsa m’madzi ambiri.+Mundilanditse m’manja mwa anthu achilendo,+   Anthu amene amalankhula zinthu zonama,+Amenenso dzanja lawo lamanja limachita zachinyengo.+   Inu Mulungu, ine ndidzakuimbirani nyimbo yatsopano.+Ndidzaimba nyimbo yokutamandani ndi choimbira cha zingwe 10.+ 10  Ndidzaimbira inu amene mumapulumutsa mafumu,+Amene mumalanditsa ine Davide mtumiki wanu ku lupanga lovulaza.+ 11  Ndimasuleni ndi kundilanditsa m’manja mwa anthu achilendo,+Anthu amene amalankhula zinthu zonama,+Amenenso dzanja lawo lamanja limachita zachinyengo.+ 12  Anthuwo amanena kuti: “Ana athu aamuna, mu unyamata wawo, ali ngati mitengo imene yangokhwima kumene,+Ndipo ana athu aakazi ali ngati mizati yapakona yosemedwa mwaluso ya m’nyumba ya mfumu. 13  Nkhokwe zathu ndi zodzaza ndi zakudya zosiyanasiyana.+Nkhosa zathu zikuswana kukhala masauzandemasauzande. Nkhosa imodzi ikukhala masauzande 10 m’misewu. 14  Ng’ombe zathu zili ndi bere, sizikuvulala kapena kubereka ana akufa,+Ndipo palibe munthu amene akulira m’mabwalo athu.+ 15  Odala ndi anthu amene zimenezi zikuwachitikira.”Ayi, koma odala ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.+

Mawu a M'munsi