Salimo 114:1-8
114 Pamene Isiraeli anatuluka mu Iguputo,+Pamene nyumba ya Yakobo inatuluka pakati pa anthu olankhula zosamveka,+
2 Yuda anakhala malo ake oyera,+Ndipo Isiraeli anakhala ufumu wake waukulu.+
3 Nyanja inaona ndipo inathawa.+Yorodano anabwerera m’mbuyo.+
4 Mapiri anadumphadumpha ngati nkhosa zamphongo,+Zitunda zinadumphadumpha ngati ana a nkhosa.
5 Kodi chinavuta n’chiyani nyanja iwe kuti uthawe?+Kodi iwe Yorodano chinavuta n’chiyani kuti ubwerere m’mbuyo?+
6 Nanga inu mapiri, chinavuta n’chiyani kuti mudumphedumphe ngati nkhosa zamphongo?+Inunso zitunda, chinavuta n’chiyani kuti mudumphedumphe ngati ana a nkhosa?+
7 Chifukwa cha Ambuye, chita mantha aakulu dziko lapansi iwe,+Chita mantha aakulu chifukwa cha Mulungu wa Yakobo,
8 Amene amasintha thanthwe kukhala dambo la madzi,+Ndiponso amasintha mwala wa nsangalabwi kukhala kasupe.+