Salimo 73:1-28

Nyimbo ya Asafu.+ 73  Mulungu ndi wabwinodi kwa Isiraeli, kwa anthu oyera mtima.+   Koma ine phazi langa linangotsala pang’ono kupatuka,+Mapazi anga anangotsala pang’ono kuterereka.+   Pakuti ndinachitira nsanje anthu odzitukumula,+Ndikamaona mtendere wa anthu oipa.+   Pakuti samva zowawa za imfa.+Ndipo mimba zawo ndi zazikulu chifukwa cha kunenepa.+   Iwo sakumana ndi mavuto amene anthu onse amakumana nawo,+Ndipo sakumana ndi masoka mofanana ndi anthu ena onse.+   Choncho kudzikuza kuli ngati mkanda m’khosi mwawo,+Ndipo avala chiwawa ngati malaya.+   Diso lawo latuzuka chifukwa cha kunenepa.+Achita zambiri kuposa zolingalira za mtima wawo.+   Iwo amanyodola ndi kulankhula zinthu zoipa.+Amalankhula za chinyengo chawo modzikweza.+   Kudzikweza kwawo kwafika kumwamba,+Akuyendayenda padziko lapansi ndipo lilime lawo likunena zilizonse zimene akufuna.+ 10  Choncho woipa amatengera anthu a Mulungu kumalo omwewo,Ndipo amamwa madzi m’kapu yodzaza bwino. 11  Iwo anena kuti: “Mulungu angadziwe bwanji?+Kodi Wam’mwambamwamba akudziwa zimenezi?”+ 12  Onani! Awa ndi anthu oipa, amene akukhala mosatekeseka mpaka kalekale.+Iwo achulukitsa chuma chawo.+ 13  Ndithudi, ndayeretsa mtima wanga pachabe,+Ndipo ndasamba m’manja mwanga pachabe posonyeza kuti ndine wopanda cholakwa.+ 14  Ndinali kukumana ndi masoka tsiku lililonse,+Ndipo m’mawa uliwonse ndinali kudzudzulidwa.+ 15  Ngati ndikananena kuti: “Ndidzalankhula za zinthu zimenezi,”Pamenepo ndikanachitira chinyengoM’badwo wa ana anu aamuna.+ 16  Ndipo ndinali kuganizira nkhani imeneyi kuti ndiimvetse.+Zinali zopweteka kwa ine, 17  Kufikira pamene ndinalowa m’malo opatulika aulemerero a Mulungu.+Ndinafuna kudziwa za tsogolo lawo.+ 18  Ndithudi, mwawaimika pamalo oterera.+Mwawagwetsa kuti awonongeke.+ 19  Haa! M’kanthawi kochepa, iwo akhala chinthu chodabwitsa.+Afika pamapeto awo ndipo atha chifukwa cha masoka owagwera modzidzimutsa! 20  Inu Yehova, anthu amenewa ali ngati maloto amene aiwalika podzuka.+Choncho pamene mukuimirira mudzawakana mochititsa manyazi.+ 21  Pakuti mtima unandipweteka+Ndipo ndinamva ululu mu impso zanga.+ 22  Ndinakhala wopanda nzeru ndipo sindinadziwe kanthu.+Ndinakhala ngati nyama yakuthengo pamaso panu.+ 23  Koma ine ndili ndi inu nthawi zonse.+Mwandigwira dzanja langa lamanja.+ 24  Mudzanditsogolera ndi malangizo anu,+Ndipo pambuyo pake mudzanditenga ndi kundipatsa ulemerero.+ 25  Winanso ndani kumwambako amene ali kumbali yanga?+Palibe wina wondisangalatsa padziko lapansi koma inu nokha.+ 26  Thupi langa ndi mtima wanga zalefuka.+Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga ndiponso cholowa changa mpaka kalekale.+ 27  Pakuti onse okhala kutali ndi inu adzatheratu.+Mudzawononga ndithu aliyense wochita chigololo mwa kukusiyani.+ 28  Koma kwa ine kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino.+Yehova Ambuye Wamkulu Koposa ndiye pothawirapo panga,+Kuti ndilengeze za ntchito zanu zonse.+

Mawu a M'munsi