Salimo 6:1-10

Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe chapansipansi* ndi zoimbira za zingwe.+ Nyimbo ya Davide. 6  Inu Yehova, musandidzudzule mutakwiya.+Musandiwongolere mutapsa mtima.+   Ndikomereni mtima, inu Yehova, chifukwa ndikulefuka.+Ndichiritseni,+ inu Yehova, chifukwa mafupa anga agwedezeka.   Moyo wanga wasokonezeka kwambiri.+Kodi inu Yehova, mudzadikira kufikira liti?+   Bwererani+ mudzapulumutse moyo wanga, inu Yehova.+Ndipulumutseni chifukwa cha kukoma mtima kwanu kosatha.+   Pakuti akufa satchula za inu.+Kodi ndani angatamande inu ali m’Manda?*+   Ndalefuka chifukwa cha kuusa moyo* kwanga.+Usiku wonse ndimanyowetsa bedi langa.+Ndimakhathamitsa bedi langa ndi misozi.+   Maso anga achita mdima chifukwa cha chisoni changa.+Maso anga akalamba chifukwa cha anthu onse ondichitira zoipa.+   Ndichokereni pamaso panga inu nonse ochita zopweteka ena,+Chifukwa Yehova adzamva ndithu mawu a kulira kwanga.+   Yehova adzamva ndithu pempho langa loti andikomere mtima.+Yehova adzalandira pemphero langa.+ 10  Adani anga onse adzachita manyazi kwambiri+ ndipo adzasokonezeka.Adzabwerera, ndipo nthawi yomweyo adzachita manyazi.+

Mawu a M'munsi

N’kutheka kuti mawu amene tawamasulira kuti “chapansipansi” akutanthauza kuti anali kuimba nyimbo imeneyi motsitsa kapena mwabesi.
Onani Zakumapeto 5.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.