Salimo 115:1-18

115  Ife sitikuyenerera kalikonse, inu Yehova, ife sitikuyenerera kalikonse,+Koma dzina lanu ndi loyenera kulemekezedwa+Malinga ndi kukoma mtima kwanu kosatha, malinganso ndi choonadi chanu.+   Musalole kuti mitundu izinena kuti:+“Mulungu wawo ali kuti tsopano?”+   Koma Mulungu wathu ali kumwamba.+Chilichonse chimene anafuna kuchita anachita.+   Mafano awo ndi opangidwa ndi siliva ndi golide,+Ntchito ya manja a munthu wochokera kufumbi.+   Pakamwa ali napo koma salankhula,+Maso ali nawo koma saona.+   Makutu ali nawo koma satha kumva.+Mphuno ali nayo koma sanunkhiza.+   Manja ali nawo, koma sakhudza kanthu.+Mapazi ali nawo koma sayenda.+Satulutsa mawu ndi mmero wawo.+   Amene amawapanga adzafanana nawo.+Onse amene amawakhulupirira adzakhala ngati mafanowo.+   Iwe Isiraeli, khulupirira Yehova.+Iye ndiye thandizo lako ndi chishango chako.+ 10  Inu nyumba ya Aroni, khulupirirani Yehova.+Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.+ 11  Inu oopa Yehova, khulupirirani Yehova.+Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.+ 12  Yehova watikumbukira, ndipo adzapereka madalitso,+Adzadalitsa nyumba ya Isiraeli,+Adzadalitsa nyumba ya Aroni.+ 13  Yehova adzadalitsa anthu omuopa,+Adzadalitsa onsewo osasiyapo aliyense.+ 14  Yehova adzakuchulukitsani,+Inu ndi ana anu.+ 15  Inu ndinu amene mwadalitsidwa ndi Yehova,+Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi.+ 16  Kunena za kumwamba, kumwamba ndi kwa Yehova,+Koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.+ 17  Akufa satamanda Ya,+Ngakhalenso aliyense wotsikira kuli chete.+ 18  Koma ife tidzatamanda Ya+Kuyambira tsopano mpaka kalekale.+Tamandani Ya, anthu inu!+

Mawu a M'munsi