Salimo 41:1-13
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.
41 Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka.+Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa.+
2 Yehova adzamuteteza ndi kumusunga ali wamoyo.+Adzatchedwa wodala padziko lapansi.+Ndipo Mulungu sangamupereke kwa adani ake.+
3 Yehova adzachirikiza wonyozekayo pamene akudwala pabedi lake.+Mudzamusamalira bwino kwambiri pamene akudwala.+
4 Koma ine ndinati: “Inu Yehova, ndikomereni mtima.+Ndichiritseni, pakuti ndakuchimwirani.”+
5 Adani anga amanena zoipa zokhazokha za ine kuti:+“Kodi ameneyu afa liti kuti dzina lake lifafanizike?”
6 Wina akabwera kudzandiona, amalankhula zabodza kuchokera mumtima mwake.+Amasonkhanitsa nkhani zoipa.Akatero amachoka, ndipo kunjako amauza ena zabodza zokhudza ine.+
7 Mogwirizana, onse amene amadana nane amanong’onezana kuti andiukire.+Amandikonzera chiwembu kuti andichitire zinthu zoipa. Iwo amati:+
8 “Amutsanulira tsoka.*+Tsopano popeza iye wagona, sadzukanso.”+
9 Koma munthu amene ndinali kukhala naye mwamtendere, amene ndinali kumukhulupirira,+Munthu amene anali kudya chakudya changa,+ wakweza chidendene chake kundiukira.+
10 Koma inu Yehova, ndikomereni mtima ndi kundidzutsa,+Kuti ndiwabwezere.+
11 Mukatero ndidziwa kuti mwasangalala nane,Chifukwa mdani wanga sadzafuula mosangalala kuti wandipambana.+
12 Koma ine mwandichirikiza chifukwa cha mtima wanga wosagawanika,+Ndipo mudzandiika pamaso panu mpaka kalekale.+
13 Adalitsike Yehova Mulungu wa Isiraeli,+Kuyambira kalekale mpaka kalekale.+Ame! Ame!*+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “chinthu chopanda pake.”
^ Kapena kuti “Zikhale momwemo! Zikhale momwemo!”