Salimo 40:1-17

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide. 40  Ndinayembekezera Yehova ndi mtima wonse,+Choncho iye anatchera khutu kwa ine ndipo anamva kufuula kwanga kopempha thandizo.+   Iye ananditulutsanso m’dzenje la madzi a mkokomo,+Ananditulutsa m’chithaphwi cha matope.+Kenako anapondetsa phazi langa pathanthwe.+Anandiyendetsa panthaka yolimba.+   Komanso anaika mawu a nyimbo yatsopano m’kamwa mwanga,Nyimbo yotamanda Mulungu wathu.+Ambiri adzaona zimenezi ndipo adzachita mantha,+Iwo adzakhulupirira Yehova.+   Wodala ndi munthu wamphamvu amene amakhulupirira Yehova,+Munthu amene sanacheukire anthu otsutsa,Kapena anthu amene anapatukira m’njira za mabodza.+   Inu Yehova Mulungu wanga, mwatichitira zinthu zambiri zodabwitsa,+Ndipo mumatiganizira.+Palibe angafanane ndi inu.+Ndikafuna kulankhula ndi kunena za zodabwitsazo,Zimachuluka kwambiri moti sindingathe kuzifotokoza.+   Nsembe ndiponso zopereka, simunasangalale nazo.+Inu munatsegula makutu anga.+Simunapemphe nsembe yopsereza ndi nsembe yamachimo.+   Chifukwa cha zimenezo ndinati: “Ine ndabwera,+Pakuti mumpukutu munalembedwa za ine.+   Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga,+Ndipo chilamulo chanu chili mumtima mwanga.+   Ndanena za uthenga wabwino wachilungamo mumpingo waukulu.+Onani! Sindinatseke pakamwa panga.+Inu Yehova, mukudziwa bwino zimenezi.+ 10  Chilungamo chanu sindinachibise mumtima mwanga.+Ndinalengeza za kukhulupirika kwanu ndi chipulumutso chanu.+Sindinabise kukoma mtima kwanu kosatha ndi choonadi chanu mumpingo waukulu.”+ 11  Inu Yehova, musasiye kundimvera chisoni.+Kukoma mtima kwanu kosatha komanso choonadi chanu zinditeteze nthawi zonse.+ 12  Pakuti masoka anandizungulira moti sindinathe kuwawerenga.+Zolakwa zanga zochuluka zinandifikira modzidzimutsa moti sindinathe kuziona mmene zinachulukira.+Zinachuluka kwambiri kuposa tsitsi la kumutu kwanga,+Ndipo ndinataya mtima.+ 13  Khalani wofunitsitsa kundilanditsa, inu Yehova.+Inu Yehova, fulumirani kundithandiza.+ 14  Onse amene akufunafuna moyo wanga kuti aufafanize+Achite manyazi ndi kuthedwa nzeru.+Amene akukondwera ndi tsoka langa abwerere ndipo anyazitsidwe.+ 15  Onse amene akunena kuti: “Eyaa! Eyaa!”+Ayang’anitsitse modabwa chifukwa cha manyazi awo.+ 16  Onse amene akufunafuna inu,+Akondwere ndi kusangalala mwa inu.+Onse amene amakonda chipulumutso chanu,+Nthawi zonse azinena kuti: “Yehova alemekezeke.”+ 17  Koma ine ndasautsika ndipo ndasauka.+Yehova amandiwerengera.+Inu ndinu thandizo langa ndi Wopereka chipulumutso kwa ine.+Inu Mulungu wanga musachedwe.+

Mawu a M'munsi