Salimo 49:1-20
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+
49 Mvetserani izi, anthu nonsenu.Tcherani khutu inu nonse a m’nthawi* ino,+
2 Inu mtundu wa anthu ndiponso inu ana a anthu,Inu olemera pamodzi ndi inu osauka.+
3 Pakamwa panga padzalankhula zinthu zanzeru,+Ndipo zosinkhasinkha za mtima wanga zidzakhala zinthu zakuya.+
4 Ndidzatchera khutu kuti ndimvetsere mwambi.+Poimba zeze ndidzamasulira mawu anga ophiphiritsa.+
5 Ndichitirenji mantha m’masiku oipa,+Pamene zolakwa za ofuna kundigwetsa zandizinga?+
6 Anthu amene akukhulupirira chuma chawo,+Amene akudzitamandira chifukwa cha kuchuluka kwa chuma chawo,+
7 Palibe ngakhale mmodzi wa iwo amene angathe kuwombola m’bale wake,+Kapena kumuperekera dipo* kwa Mulungu,
8 (Ndipo malipiro owombolera moyo wawo ndi amtengo wapatali,+Moti munthu sangathe kuwapereka mpaka kalekale)
9 Kuti akhale ndi moyo mpaka muyaya osaona dzenje la manda.+
10 Pakuti amaona kuti ngakhale anthu anzeru amafa,+Wopusa ndi wopanda nzeru, onsewo amawonongeka,+Ndipo chuma chawo amasiyira anthu ena.+
11 Zokhumba za mtima wawo n’zakuti nyumba zawo zikhalebe mpaka kalekale,+Mahema awo akhalebe ku mibadwomibadwo.+Malo awo amawatcha mayina awo.+
12 Komabe munthu wochokera kufumbi, ngakhale atakhala wolemekezeka, sangakhale ndi moyo mpaka kalekale.+Iye amangofanana ndi nyama zimene zaphedwa.+
13 Umu ndi mmene zimakhalira ndi zitsiru,+Komanso amene amazitsanzira, omwe amasangalala ndi mawu awo odzitukumula. [Seʹlah.]
14 Awatsogolera ku Manda ngati nkhosa zopita kokaphedwa.+Imfa idzakhala m’busa wawo.+Ndipo m’mawa anthu owongoka mtima adzawalamulira.+Matupi awo adzawonongeka.+Aliyense wa iwo malo ake okhala ndi ku Manda, osati malo okwezeka.+
15 Koma Mulungu adzawombola moyo wanga ku Manda,+Pakuti adzandilandira. [Seʹlah.]
16 Musachite mantha chifukwa chakuti munthu wina akupeza chuma,+Kapena chifukwa chakuti ulemerero wa nyumba yake ukuwonjezeka,+
17 Pakuti pa imfa yake sangatenge kena kalikonse.+Ulemerero wake sudzapita naye pamodzi.+
18 Pakuti pamene anali moyo anali kutamanda moyo wake,+(Ndipo anthu adzakutamanda chifukwa chakuti walemera)+
19 Moyo wake udzafanana ndi wa m’badwo wa makolo ake.+Ndipo iwo sadzaonanso kuwala.+
20 Munthu, ngakhale atakhala wolemekezeka, koma ngati ali wosazindikira,+Amangofanana ndi nyama zimene zaphedwa.+