Salimo 57:1-11

Kwa wotsogolera nyimbo. “Musandiwononge.” Salimo la Davide. Mikitamu.* Pa nthawi imene anathawa Sauli n’kukalowa m’phanga.+ 57  Ndikomereni mtima inu Mulungu, ndikomereni mtima,+Pakuti ine ndathawira kwa inu.+Ndipo ndathawira mumthunzi wa mapiko anu kufikira masoka atadutsa.+   Ndikufuulira Mulungu Wam’mwambamwamba, Mulungu woona amene akuthetsa masoka amenewa kuti zinthu zindiyendere bwino.+   Adzatumiza thandizo kuchokera kumwamba ndi kundipulumutsa.+Adzasokoneza wofuna kundiwakha ndi pakamwa pake.+ [Seʹlah.]Mulungu adzasonyeza kukoma mtima kwake kosatha ndi choonadi chake.+   Moyo wanga uli pakati pa mikango.+Sindingachitire mwina koma kugona pakati pa ana a anthu, amene ali ngati nyama zoopsa zodya anthu,Amene mano awo ali ngati mikondo ndi mivi,+Ndipo lilime lawo lili ngati lupanga lakuthwa.+   Inu Mulungu, kwezekani kupitirira kumwamba.+Ulemerero wanu ukhale pamwamba pa dziko lonse lapansi.+   Iwo anditchera ukonde panjira yanga.+Moyo wanga wagwidwa ndi chisoni.+Andikumbira mbuna.Koma iwo agweramo.+ [Seʹlah.]   Mtima wanga wakhazikika, Inu Mulungu,+Mtima wanga wakhazikika.Ndidzaimba nyimbo zokutamandani.+   Iwe mtima wanga, galamuka.+Iwe choimbira cha zingwe, galamuka, ndi iwenso zeze.+Ndidzadzuka m’bandakucha usanafike.   Ndidzakutamandani pakati pa mitundu ya anthu, inu Yehova.+Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa mitundu ya anthu.+ 10  Pakuti kukoma mtima kwanu kosatha n’kwakukulu ndipo kwafika kumwamba,+Choonadi chanu chafika kuthambo.+ 11  Inu Mulungu, kwezekani kupitirira kumwamba.+Ulemerero wanu ukhale pamwamba pa dziko lonse lapansi.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 16:Kamutu.