Salimo 136:1-26

136  Yamikani Yehova anthu inu, pakuti iye ndi wabwino:+Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+   Yamikani Mulungu wa milungu:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+   Yamikani Mbuye wa ambuye:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+   Yamikani Wochita zodabwitsa ndiponso ntchito zazikulu:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+   Yamikani amene anapanga kumwamba mwanzeru:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+   Yamikani woyala dziko lapansi pamwamba pa madzi:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+   Yamikani wopanga zounikira zazikulu:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+   Amenenso anapanga dzuwa kuti lizilamulira masana:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+   Amene anapanga mwezi ndi nyenyezi kuti zizilamulira pamodzi usiku:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 10  Yamikani amene anakantha Aiguputo mwa kupha ana awo oyamba kubadwa:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 11  Yamikani amene anatulutsa Aisiraeli pakati pawo:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 12  Anawatulutsa ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasula:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale. 13  Yamikani amene anagawa pakati Nyanja Yofiira:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 14  Amenenso anachititsa Isiraeli kudutsa pakati pake:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 15  Amenenso anakutumulira Farao ndi gulu lake lankhondo m’Nyanja Yofiira:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 16  Yamikani amene anayendetsa anthu ake m’chipululu:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 17  Yamikani amene anapha mafumu amphamvu:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 18  Amenenso anapha mafumu olemekezeka:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 19  Iye anapha Sihoni mfumu ya Aamori:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 20  Anaphanso Ogi mfumu ya Basana:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 21  Ndipo dziko lawo analipereka kwa anthu ake kukhala cholowa:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 22  Cholowa cha Isiraeli mtumiki wake:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 23  Iye amene anatikumbukira pamene adani anatinyazitsa:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 24  Amene anatipulumutsa mobwerezabwereza kuchokera m’manja mwa adani athu:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 25  Amenenso amapereka chakudya kwa zamoyo zonse:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 26  Yamikani Mulungu wakumwamba:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

Mawu a M'munsi