Salimo 28:1-9

Salimo la Davide. 28  Ndikuitana inu Yehova.+Inu Thanthwe langa, musatseke makutu anu pamene ine ndikuitana,+Kuti musakhale chete pamaso panga,+Kutinso ine ndisafanane ndi amene akutsikira kudzenje la manda.+   Imvani mawu anga ochonderera pamene ndikufuulira inu kuti mundithandize,Pamene ndikukweza manja anga,+ nditayang’ana kumene kuli chipinda chamkati cha m’malo anu opatulika.+   Musandikokolole pamodzi ndi anthu oipa komanso anthu amene amachita zopweteka anzawo,+Anthu amene amalankhula mawu amtendere ndi anzawo+ koma m’mitima yawo muli zinthu zoipa.+   Muwabwezere mogwirizana ndi zochita zawo,+Mogwirizana ndi kuipa kwa zochita zawo.+Abwezereni mogwirizana ndi ntchito za manja awo.+Abwezereni zochita zawo.+   Pakuti iwo salabadira zochita za Yehova,+Kapena ntchito za manja ake.+Mulungu sadzawamanga koma adzawapasula.   Adalitsike Yehova, chifukwa wamva kuchonderera kwanga.+   Yehova ndiye mphamvu yanga+ ndi chishango changa.+Mtima wanga umam’khulupirira.+Iye wandithandiza, moti mtima wanga ukukondwera.+Ndidzamutamanda mwa kumuimbira nyimbo yanga.+   Yehova ndiye mphamvu kwa anthu ake,+Iye ndi malo achitetezo odzetsa chipulumutso chachikulu kwa wodzozedwa wake.+   Pulumutsani anthu anu, ndipo dalitsani cholowa chanu.+Mukhale m’busa wawo ndipo muwanyamule mpaka kalekale.+

Mawu a M'munsi