Salimo 81:1-16
Kwa wotsogolera nyimbo pa Gititi.*+ Salimo la Asafu.
81 Anthu inu, fuulani mosangalala kwa Mulungu amene ndi mphamvu yathu,+Fuulirani Mulungu wa Yakobo mosangalala chifukwa wapambana.+
2 Yambani kuimba nyimbo+ ndipo tengani maseche,+Zeze womveka mosangalatsa pamodzi ndi choimbira cha zingwe.+
3 Pa tsiku lokhala mwezi, imbani lipenga la nyanga ya nkhosa.+Pa tsiku looneka mwezi wathunthu, imbani lipenga la nyanga ya nkhosa, loimba pa tsiku la chikondwerero.+
4 Pakuti limeneli ndi lamulo kwa Isiraeli,+Komanso chigamulo cha Mulungu wa Yakobo.
5 Anaika chigamulocho monga chikumbutso kwa Yosefe,+Pamene anali kutuluka m’dziko la Iguputo.+Ndinali kumva chilankhulo chimene sindinali kuchidziwa.+
6 Mulungu akuti: “Ndinachotsa goli paphewa lake.+Manja ake anamasuka ndipo sananyamule dengu.+
7 Pa nthawi ya nsautso unaitana ndipo ine ndinakupulumutsa.+Ndinayamba kukuyankha m’malo obisika a bingu.+Ndinakusanthula pamadzi a Meriba.+ [Seʹlah.]
8 Imvani anthu anga, ndipo ndidzakulangizani ndi kukuchenjezani.+Zikanakhala bwino ngati mukanandimvera, inu Aisiraeli.+
9 Pakati panu sipadzakhala mulungu wosadziwika.+Ndipo simudzagwadira mulungu wachilendo.+
10 Ine Yehova, ndine Mulungu wanu,+Amene ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo.+Tsegulani pakamwa panu ndipo ndidzaikamo chakudya.+
11 Koma anthu anga sanamvere mawu anga.+Ndipo Isiraeli sanasonyeze kuti ndi wofunitsitsa kundimvera.+
12 Choncho ndinawasiya kuti apitirize kuumitsa mtima wawo.+Iwo anapitiriza kuyenda mu nzeru zawo.+
13 Haa! Zikanakhala bwino ngati anthu anga akanandimvera,+Zikanakhala bwino ngati Isiraeli akanayenda m’njira zanga.+
14 Ndikanagonjetsa adani awo mosavuta,+Ndipo ndikanalanga adani awo ndi dzanja langa.+
15 Koma odana kwambiri ndi Yehova adzabwera kwa iye akunjenjemera ndi mantha,+Ndipo nthawi yawo idzakhala mpaka kalekale.
16 Ine ndidzadyetsa Aisiraeli tirigu wabwino koposa,+Ndipo ndidzawapatsa uchi wochokera pathanthwe+ kuti adye ndi kukhuta.”