Salimo 127:1-5
Nyimbo ya Solomo Yokwerera Kumzinda.
127 Yehova akapanda kumanga nyumba,+Omanga nyumbayo amagwira ntchito pachabe.+Yehova akapanda kulondera mzinda,+Alonda amakhala maso pachabe.+
2 Anthu inu mukudzuka m’mawa pachabe,+Mukungovutika kugwira ntchito mpaka usiku,+Mukudya chakudya chimene mwachipeza movutikira.+Koma Mulungu amapereka tulo kwa wokondedwa wake.+
3 Taonani! Ana ndi cholowa chochokera kwa Yehova.+Chipatso cha mimba ndicho mphoto.+
4 Ana a bambo wachinyamata+Ali ngati mivi m’dzanja la mwamuna wamphamvu.+
5 Wodala ndi mwamuna wamphamvu amene wadzaza+ kachikwama kake ka mivi ndi mivi imeneyo.Abambo oterowo sadzachita manyazi,+Pakuti anawo adzalankhula ndi adani pachipata.