Salimo 29:1-11
Salimo la Davide.
29 M’patseni Yehova, inu amphamvu,*M’patseni Yehova ulemerero ndipo vomerezani kuti iye ndi wamphamvu.+
2 M’patseni Yehova ulemerero woyenera dzina lake.+Weramirani Yehova mutavala zovala zopatulika zokongola.+
3 Liwu la Yehova lili pamwamba pa madzi,*+Liwu la Mulungu waulemerero+ lagunda ngati bingu.+Yehova ali pamwamba pa madzi ambiri.+
4 Liwu la Yehova ndi lamphamvu,+Liwu la Yehova ndi lokwezeka.+
5 Liwu la Yehova likuthyola mitengo ya mkungudza,Yehova akuthyolathyola mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni.+
6 Iye akuichititsa kudumphadumpha ngati mwana wa ng’ombe,+Lebanoni ndi Sirioni+ akudumphadumpha ngati ana a ng’ombe zakutchire.
7 Liwu la Yehova likutulutsa malawi a moto.+
8 Liwu la Yehova likuchititsa chipululu kuphiriphitha,+Yehova akuchititsa chipululu cha Kadesi+ kuphiriphitha.
9 Liwu la Yehova likuchititsa mbawala zazikazi kuphiriphitha ndi ululu wa pobereka,+Ndipo likufafaniza nkhalango.+M’kachisi wake aliyense akunena kuti: “Ulemerero ndi wa Mulungu!”+
10 Yehova wakhala pampando wake wachifumu pamwamba pa chigumula,*+Ndipo Yehova ndi mfumu mpaka kalekale.+
11 Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu.+Yehova adzadalitsa anthu ake ndi mtendere.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “ana a amphamvu.”
^ “Madzi” amenewa akutanthauza “mvula yamkuntho.”
^ Kapena kuti “pamwamba pa nyanja yaikulu ya kumwamba.”