Salimo 55:1-23
Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Masikili.* Salimo la Davide.
55 Inu Mulungu, mvetserani pemphero langa.+Musanyalanyaze pempho langa lakuti mundikomere mtima.+
2 Ndimvetsereni mwatcheru ndi kundiyankha.+Mtima wanga suli m’malo chifukwa cha mavuto anga,+Sindingachitire mwina koma kusonyeza nkhawa zanga,
3 Chifukwa cha zimene adani akunena, ndiponso chifukwa chakuti oipa andipanikiza.+Pakuti akundikhuthulira mavuto,+Ndipo mwaukali akundisungira chidani.+
4 Mtima wanga ukundipweteka kwambiri.+Ndipo ndikuopa imfa.+
5 Ndagwidwa ndi mantha ndipo ndikunjenjemera.+Inde ndikunthunthumira.
6 Ndipo ndikunena kuti: “Ndikanakhala ndi mapiko ngati njiwa!+Ndikanauluka ndi kukakhala kwina.+
7 Ndikanathawira kutali.+Ndikanapita kukakhala m’chipululu.+ [Seʹlah.]
8 Ndikanathawira kumalo opulumukirako,Kuthawa mphepo yamphamvu, ndithu kuthawa mphepo yamkuntho.”+
9 Inu Yehova, sokonezani anthu oipa, ndipo sokonezani zonena zawo,+Pakuti ndaona ziwawa ndi mikangano mumzinda.+
10 Usana ndi usiku amayenda pamwamba pa mpanda kuzungulira mzindawo.+Ndipo mumzindawo muli zopweteka ndi masautso.+
11 Mmenemo muli mavuto okhaokha.Ndipo kuponderezana ndi chinyengo sizinachoke kubwalo la mzindawo.+
12 Pakuti amene ananditonza si mdani.+Akanakhala mdani ndikanapirira.Amene anadzikweza pamaso panga si munthu wodana nane kwambiri.+Akanakhala munthu wodana nane kwambiri ndikanabisala.+
13 Koma ndiwe, munthu wofanana ndi ine,+Munthu amene ndimam’dziwa bwino ndiponso mnzanga weniweni,+
14 Chifukwa tinali mabwenzi apamtima.+Tinali kuyenda limodzi ndi khwimbi la anthu kupita kunyumba ya Mulungu.+
15 Chiwonongeko chiwagwere!+Atsikire ku Manda ali amoyo.+Pakuti kulikonse kumene apita, zinthu zoipa zimakhala mumtima mwawo.+
16 Koma ine ndidzafuulira Mulungu.+Ndipo Yehova adzandipulumutsa.+
17 Usiku, m’mawa ndi masana ndimakhala ndi nkhawa ndipo ndimakhala ndikulira,+Choncho Mulungu amamva mawu anga.+
18 Iye adzandiwombola ndi kundikhazika pa mtendere, kundichotsa pankhondo,+Pakuti khamu la anthu landiukira.+
19 Mulungu amene wakhala pampando wachifumu kuyambira kalekale,+Adzandimvera ndipo adzawayankha,+ [Seʹlah.]Anthu osafuna kusintha makhalidwe awo oipa,+Ndiponso amene saopa Mulungu.+
20 Iye watambasula dzanja lake kuukira anthu amene ali naye pa mtendere.+Wanyoza pangano lake.+
21 Mawu a pakamwa pake ndi osalala ngati mafuta a mkaka,+Koma mtima wake umakonda ndewu.+Mawu ake ndi osalala ngati mafuta,+Koma ali ngati lupanga lakuthwa.+
22 Umutulire Yehova nkhawa zako,+Ndipo iye adzakuchirikiza.+Sadzalola kuti wolungama agwedezeke.+
23 Koma inu Mulungu, mudzatsitsira oipa kumanda.+Ndipo anthu amene ali ndi mlandu wa magazi komanso anthu achinyengo, sadzakwanitsa kukhala ngakhale hafu ya moyo wawo.+Koma ine ndidzakhulupirira inu.+