Salimo 125:1-5
Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
125 Okhulupirira Yehova+Ali ngati phiri la Ziyoni,+ limene silingagwedezeke, koma lidzakhalapo mpaka kalekale.+
2 Yehova wazungulira anthu ake+Ngati mmene mapiri azungulirira Yerusalemu,+Kuyambira tsopano mpaka kalekale.+
3 Ndodo yachifumu ya oipa sidzapitiriza kukhala+ padziko limene olungama analandira monga cholowa chawo,Kuti olungamawo asatambasule dzanja lawo ndi kuchita choipa.+
4 Inu Yehova, chitirani zabwino anthu abwino,+Anthu owongoka mtima.+
5 Koma anthu obwerera kunjira zawo zokhotakhota,+Yehova adzawapereka ku chilango pamodzi ndi ochita zopweteka anzawo.+Ndipo mu Isiraeli mudzakhala mtendere.+