Salimo 42:1-11

Kwa wotsogolera nyimbo. Masikili* ya ana a Kora.+ 42  Monga mmene mbawala yaikazi imalakalakira mitsinje ya madzi,Moyo wanganso ukulakalaka inu Mulungu wanga.+   Moyo wanga ukulakalaka Mulungu,+ ukulakalaka Mulungu wamoyo.+Ndidzapita liti kunyumba ya Mulungu kukaonekera pamaso pake?+   Misozi yanga yasanduka chakudya changa usana ndi usiku,+Pamene anthu akundifunsa tsiku lonse kuti: “Mulungu wako ali kuti?”+   Ndidzakumbukira zinthu zakale ndipo moyo wanga udzavutika pokumbukira zimenezo.+Pakuti ndinali kuyenda ndi khwimbi la anthu,Ndinali kuyenda pang’onopang’ono patsogolo pawo kupita kunyumba ya Mulungu,+Tinali kufuula mosangalala ndi kuyamika Mulungu.+Khamu la anthu okondwerera madyerero linali kunditsatira.+   N’chifukwa chiyani ukutaya mtima, moyo wangawe?+Ndipo n’chifukwa chiyani ukusautsika mkati mwanga?+Yembekezera Mulungu,+Ndipo ndidzamutamanda pakuti iye ndiye mpulumutsi wanga wamkulu.+   Inu Mulungu wanga, ine ndataya mtima.+N’chifukwa chake ndakumbukira inu,+Pamene ndili m’dziko la Yorodano ndi m’mapiri a Herimoni,+Pamene ndili m’phiri laling’ono.+   Madzi akuya akufuulira madzi akuya,Kudzera mu mkokomo wa madzi otumphuka.Mafunde anu onse amphamvu,+Andimiza.+   Masana Yehova adzalamula kukoma mtima kwake kosatha kuti kufike pa ine,+Ndipo usiku ndidzaimba za iye.+Ndidzapemphera kwa Mulungu wondipatsa moyo.+   Ndidzauza Mulungu, thanthwe langa kuti:+“N’chifukwa chiyani mwandiiwala?+Ndikuyenderanji wachisoni chifukwa choponderezedwa ndi mdani wanga?”+ 10  Odana nane akunditonza kwambiri moti zikungokhala ngati mafupa anga aphwanyidwa,+Pakuti anthu akundifunsa tsiku lonse kuti: “Mulungu wako ali kuti?”+ 11  N’chifukwa chiyani ukutaya mtima, moyo wangawe?+Ndipo n’chifukwa chiyani ukusautsika mkati mwanga?+Yembekezera Mulungu,+Ndipo ndidzamutamanda pakuti iye ndiye mpulumutsi wanga wamkulu ndiponso ndiye Mulungu wanga.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.