Salimo 12:1-8

Kwa wotsogolera nyimbo: Iimbidwe chapansipansi.*+ Nyimbo ya Davide. 12  Ndipulumutseni,+ inu Yehova, pakuti anthu okhulupirika atha.+Anthu okhulupirika atheratu pakati pa ana a anthu.   Iwo amalankhulana zabodza.+Amalankhulana ndi milomo yoshashalika+ komanso ndi mitima iwiri.+   Yehova adzadula milomo yonse yolankhula zachinyengoNdi lilime lolankhula modzikuza.+   Iye adzadula anthu onena kuti: “Ndi lilime lathu tidzapambana.+Timalankhula chilichonse chimene tikufuna ndi milomo yathu. Ndani angatilamulire?”   Tsopano Yehova wanena kuti: “Chifukwa cha kuponderezedwa kwa osautsika, chifukwa cha kuusa moyo kwa anthu osauka,+Ndidzanyamuka pa nthawiyo,+Ndidzawateteza kwa aliyense wowanyodola.”+   Mawu a Yehova ndi oyengeka bwino,+Ngati siliva woyengedwa nthawi zokwanira 7 mung’anjo ya m’nthaka.   Inu Yehova mudzawayang’anira.+Aliyense wa iwo mudzamuteteza ku m’badwo uwu mpaka kalekale.   Anthu oipa akuyendayenda ponseponse,Chifukwa ana a anthu amayamikira zoipa.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 6:Kamutu.