Salimo 18:1-50

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la mtumiki wa Yehova, Davide, amene anauza Yehova mawu a m’nyimbo iyi pa tsiku limene Yehova anamulanditsa m’manja mwa adani ake onse komanso m’manja mwa Sauli.+ Iye anati: 18  Ndidzakukondani inu Yehova, mphamvu yanga.+   Yehova ndiye thanthwe langa, malo anga achitetezo ndiponso Wopereka chipulumutso kwa ine.+Mulungu wanga ndiye thanthwe langa. Ine ndidzathawira kwa iye.+Iye ndiye chishango changa, nyanga* yanga ya chipulumutso ndiponso ndiye malo anga okwezeka achitetezo.+   Ndidzaitanira pa Yehova, Iye woyenera kutamandidwa,+Ndipo adzandipulumutsa kwa adani anga.+   Zingwe za imfa zinandikulunga,+Chikhamu cha anthu opanda pake chinali kundiopseza.+   Zingwe za Manda zinandizungulira.+Ndinayang’anizana ndi misampha ya imfa.+   Pa nthawi ya zowawa zanga ndinaitana Yehova,Ndinafuulira Mulungu wanga kuti andithandize.+Iye anamva mawu anga ali m’kachisi wake.+Pamenepo makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.+   Dziko lapansi linayamba kugwedezekera uku ndi uku ndiponso kutekeseka.+Maziko a mapiri anagwedezeka,+Anagwedezekera uku ndi uku chifukwa Mulungu anakwiya.+   Utsi unatuluka m’mphuno mwake, ndipo moto wotuluka m’kamwa mwake unanyeketsa.+Makala onyeka anatuluka mwa iye.   Iye anaweramitsa kumwamba n’kutsika.+Mdima wandiweyani unali kunsi kwa mapazi ake. 10  Iye anafika atakwera pakerubi wouluka.+Mulungu anali kuuluka mwaliwiro pamapiko a cholengedwa chauzimu.*+ 11  Kenako anapanga mdima kukhala malo ake obisalamo,+Panali madzi akuda ndi mtambo wakuda,Zimene zinamuzungulira ngati msasa wake.+ 12  M’kuwala kochokera pamaso pake munatuluka mitambo yake,+Munatulukanso matalala ndi makala onyeka a moto.+ 13  Ali kumwamba, Yehova anayamba kugunda ngati mabingu,+Wam’mwambamwamba anayamba kutulutsa mawu ake,+Anatulutsanso matalala ndi makala onyeka a moto. 14  Anayamba kuponya mivi kuti awabalalitse.+Anaponya mphezi kuti awasokoneze.+ 15  Ndipo ngalande za pansi pa madzi zinaonekera,+Maziko a dziko lapansi anakhala poonekera.+Zinatero chifukwa cha kudzudzula kwanu, inu Yehova, chifukwa cha mphamvu ya mpweya wa m’mphuno mwanu.+ 16  Anatambasula dzanja lake kuchokera kumwamba ndi kunditenga,+Anandivuula m’madzi akuya.+ 17  Anandilanditsa kwa mdani wanga wamphamvu,+Anandilanditsa kwa odana nane chifukwa anali amphamvu kuposa ine.+ 18  Adaniwo anandifikira m’tsiku la tsoka langa,+Koma Yehova anandichirikiza.+ 19  Ananditenga ndi kundiika pamalo otakasuka.+Anandipulumutsa chifukwa anakondwera nane.+ 20  Yehova amandipatsa mphoto mogwirizana ndi chilungamo changa.+Amandibwezera mogwirizana ndi kuyera kwa manja anga.+ 21  Pakuti ndasunga njira za Yehova,+Sindinachoke kwa Mulungu wanga. Ndikanatero, ndikanachita chinthu choipa.+ 22  Zigamulo zake zonse zili pamaso panga,+Ndipo malamulo ake sindidzawataya.+ 23  Ndidzakhalabe wopanda cholakwa pamaso pake,+Ndipo ndidzayesetsa kupewa kuchita cholakwa.+ 24  Yehova andibwezere mogwirizana ndi chilungamo changa,+Andibwezere mogwirizana ndi kuyera kwa manja anga pamaso pake.+ 25  Munthu wokhulupirika, mudzamuchitira mokhulupirika.+Munthu wamphamvu wopanda cholakwa, mudzamuchitira mwachilungamo.+ 26  Kwa munthu wokhalabe woyera, mudzadzisonyeza kuti ndinu woyera,+Kwa munthu wopotoka maganizo mudzadzisonyeza kuti ndinu wochenjera,+ 27  Chifukwa anthu osautsika mudzawapulumutsa,+Koma anthu odzikweza mudzawatsitsa.+ 28  Pakuti inu Yehova mudzandiyatsira nyale yanga,+Mulungu wanga adzandiunikira mu mdima.+ 29  Pakuti ndi thandizo lanu, ndingathamangitse gulu la achifwamba.+Ndi thandizo la Mulungu wanga ndingakwere khoma.+ 30  Njira ya Mulungu woona ndi yangwiro.+Mawu a Yehova ndi oyengeka bwino.+Iye ndi chishango kwa onse othawira kwa iye.+ 31  Kodi pali Mulungu winanso woposa Yehova?+Kodi pali thanthwe linanso loposa Mulungu wathu?+ 32  Mulungu woona Ndiye amandilimbitsa,*+Ndipo adzasalaza njira yanga.+ 33  Iye adzachititsa mapazi anga kukhala aliwiro ngati a mbawala zazikazi,+Ndipo adzandiimiritsabe pamalo okwezeka kwa ine.+ 34  Iye akuphunzitsa manja anga kumenya nkhondo,+Ndipo manja anga akukunga uta wamkuwa.+ 35  Inu mudzandipatsa chishango chanu cha chipulumutso,+Dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza,+Ndipo kudzichepetsa kwanu n’kumene kudzandikweza.+ 36  Mudzakulitsa malo opondapo mapazi anga,+Ndipo mapazi anga sadzagwedezeka.+ 37  Ndidzathamangitsa adani anga ndi kuwapeza,Ndipo sindidzabwerera kufikira nditawawononga onse.+ 38  Ndidzawaphwanya zibenthuzibenthu kuti asadzukenso.+Ndidzawapondaponda ndi mapazi anga.+ 39  Inu mudzandiveka mphamvu kuti ndithe kumenya nkhondo.Mudzakomola ondiukira.+ 40  Koma mudzachititsa adani anga kugonja* pamaso panga,+Anthu odana nane kwambiri, ndidzawakhalitsa chete.+ 41  Adzafuula kupempha thandizo, koma sipadzapezeka wowapulumutsa,+Adzafuulira Yehova, koma sadzawayankha.+ 42  Ndidzawapera kukhala ngati fumbi louluzika ndi mphepo.+Ndidzawakhuthula ngati matope a mumsewu.+ 43  Inu mudzandipulumutsa kwa anthu a mtundu wanga onditola zifukwa.+Mudzandiika kukhala mtsogoleri wa mitundu yonse.+Anthu amene sindikuwadziwa adzanditumikira.+ 44  Anthu akangomva mphekesera chabe zokhudza ine, adzandimvera.+Alendo adzabwera kwa ine akunthunthumira.+ 45  Alendo adzatha mphamvu,Ndipo adzatuluka m’malo awo achitetezo akunjenjemera.+ 46  Yehova ndi wamoyo.+ Lidalitsike Thanthwe langa.+Mulungu wa chipulumutso changa akhale wokwezeka.+ 47  Mulungu woona ndiye Wobwezera adani anga.+Iye amagonjetsa mitundu ya anthu ndi kuiika kunsi kwa mapazi anga.+ 48  Iye amandipulumutsa kwa adani anga olusa.+Ndipo mudzandikweza pamwamba pa anthu amene amandiukira.+Mudzandilanditsa kwa munthu wachiwawa.+ 49  N’chifukwa chake ndidzakutamandani, inu Yehova pakati pa mitundu.+Ndipo ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.+ 50  Iye akuchita ntchito zazikulu za chipulumutso kwa mfumu yake,+Ndipo akusonyeza kukoma mtima kosatha kwa wodzozedwa wake,+kwa Davide ndi mbewu yake mpaka kalekale.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.
Kapena kuti “mapiko a mphepo.”
Mawu ake enieni, “amamangirira zolimba mphamvu m’chiuno mwanga.”
Kapena kuti “Mudzandipatsa kumbuyo kwa khosi la adani anga.”