Salimo 148:1-14
148 Tamandani Ya, anthu inu!+Tamandani Yehova inu okhala kumwamba.+Mutamandeni inu okhala m’mwamba.+
2 Mutamandeni, inu angelo ake onse.+Mutamandeni, inu khamu lake lonse.+
3 Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi.+Mutamandeni, inu nyenyezi zonse zowala.+
4 Mutamandeni, inu kumwamba kwa m’mwambamwamba,+Ndi inunso madzi okhala pamwamba pa miyamba.+
5 Zonsezi zitamande dzina la Yehova,+Pakuti iye analamula ndipo zinalengedwa.+
6 Amazichititsa kukhalapobe kwamuyaya, ngakhalenso mpaka kalekale.+Iye wazikhazikitsira lamulo, ndipo silidzatha.+
7 Tamandani Yehova, inu okhala padziko lapansi,+Inu zilombo za m’nyanja ndi inu nonse madzi akuya,+
8 Inu moto ndi matalala, chipale chofewa ndi utsi wakuda bii,+Iwe mphepo yamkuntho yokwaniritsa mawu ake.+
9 Mutamandeni inu mapiri ndi inu nonse zitunda,+Inu mitengo ya zipatso ndi inu nonse mitengo ya mkungudza.+
10 Inu nyama zakutchire ndi inu nonse nyama zoweta,+Inu zinthu zokwawa ndi mbalame zamapiko.+
11 Mutamandeni inu mafumu a padziko lapansi+ ndi inu nonse mitundu ya anthu,Inunso akalonga+ ndi inu nonse oweruza a padziko lapansi,+
12 Inu anyamata+ ndi inunso anamwali,+Inu okalamba+ pamodzi ndi ana.+
13 Onse, anthu ndi nyama, atamande dzina la Yehova,+Pakuti dzina lake lokhalo lili pamwamba posafikirika.+Ulemerero wake uli pamwamba kuposa dziko lapansi ndi kumwamba.+
14 Iye adzakweza nyanga* ya anthu ake.+Adzachititsa kuti anthu ake onse okhulupirika atamandike,+Amene ndi ana a Isiraeli, anthu amene ali pafupi ndi iye.+Tamandani Ya, anthu inu!+