Salimo 19:1-14

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. 19  Zakumwamba zikulengeza ulemerero wa Mulungu.+Ndipo m’mlengalenga mukufotokoza ntchito ya manja ake.+   Tsiku lililonse limanena mawu,+Ndipo usiku uliwonse umasonyeza nzeru.+   Sizilankhula, kapena kutulutsa mawu.Mawu awo samveka.+   Zingwe zawo zoyezera zafika padziko lonse lapansi,+Mawu awo amveka kumalekezero a dziko lapansi kumene kuli anthu.+Kumwambako Mulungu wamangira dzuwa hema.+   Dzuwalo limaoneka ngati mkwati amene akutuluka m’chipinda chake,+Limakondwa ngati mmene mwamuna wamphamvu amachitira akamathamanga m’njira.+   Limatuluka kuchokera kumalekezero ena a kumwamba,Ndi kuzungulira mpaka kumalekezero enanso.+Palibe chinthu chilichonse chimene sichimva kutentha kwake.+   Chilamulo+ cha Yehova ndi changwiro,+ chimabwezeretsa moyo.+Zikumbutso+ za Yehova ndi zodalirika,+ zimapatsa nzeru munthu wosadziwa zinthu.+   Malamulo+ ochokera kwa Yehova ndi olungama,+ amasangalatsa mtima.+Chilamulo+ cha Yehova ndi choyera,+ chimatsegula maso.+   Kuopa+ Yehova n’koyera, ndipo kudzakhalapo kwamuyaya.Zigamulo+ za Yehova n’zolondola,+ ndipo pa mbali iliyonse zasonyezadi kuti ndi zolungama.+ 10  N’zolakalakika kuposa golide, kuposa golide wambiri woyengeka bwino.+N’zotsekemera* kuposa uchi,+ inde kuposa uchi umene ukukha m’zisa.+ 11  Ndiponso mtumiki wanu amachenjezedwa nazo.+Munthu wosunga zigamulozo amapeza mphoto yaikulu.+ 12  Ndani angazindikire yekha zinthu zimene walakwitsa?+Mundikhululukire machimo amene ndachita mosadziwa.+ 13  Komanso mundiletse kuchita modzikuza, ine mtumiki wanu.+Musalole kuti kudzikuza kundilamulire.+Pamenepo ndidzakhala wopanda chifukwa,+Ndipo ndidzakhalabe wopanda milandu yambiri yophwanya malamulo. 14  Mawu a pakamwa panga ndi kusinkhasinkha kwa mtima wanga,+Zikukondweretseni, inu Yehova, Thanthwe langa+ ndi Wondiwombola.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “n’zonzuna.”